Tisamale pamaliro
- Category: Ndemanga
- Written by Limbani Katsache
Zovuta zikagwa, anthu abwinobwino amakhala pachisoni, ndipo iyi imakhala nyengo yowawitsa, choncho ndimalaulo kumva kuti ena akutenga siwa kukhala malo okatansa, kubera ena.
Kunena mosapsatira, kubera namfedwa ndi malodza chifukwa amakhala ali kale pachipsinjo choncho kuonjezera chipsinjo powabera n’kulakwa zedi.
Pali anthu ena, akamva kuti kwakuti kwagwa zovuta, amathamangira komweko, osati ndicholinga chokakhuza maliro koma utsinzinamtole basi. Ena amatha kufika mpaka kunyumba yachisoni, kapena kusiwa cholinga anthu awakhululukire koma pamapeto pake, amaonetsa mawanga awo a uchigandanga.
N’chifukwa chake tikuti, tonse tiyenera kusamala ngakhale pazovuta chifukwa akuba ena akhoza kutengerapo mwayi kuti misonzi isakate.
Kwa amene ali ndi khalidwe lobera anamfedwa, azindikire kuti chilango chikuwalinda, monga chikuyembekezera onse akuchita kusaweruzika.
Ulesi ndiwo umabala kuba. Nzeru zobera pamaliro, bwanji osazigwiritsa ntchito pochita ulimi wamthirira?








