Ndibwino kulemekeza chikhalidwe
- Category: Ndemanga
- Written by Nation Online
Mtundu ulionse uli ndi chikhalidwe chake. Ndipo pakati pa anthu a mitundu onse pamakhala zoyenera kuchita ndinso zimene munthu ukachita umakhala mlandu.
Kupanda kutsatira malamulo, ngakhale osachita kulembedwa pakati pa anthu kumadzetsa zilango.
Pakati pa Achewa, gulewamkulu ndi chimodzi mwa zinthu zaulemu kwambiri.
Tikuona kuti anthu amene adalanga mkulu amene amayesera gulewamkulu ngakhale dambwe lidali lotseka adatero chifukwa adakhala ngati mkuluyo waasusula pachilonda.
Nchifukwa chake ngakhale kuchilendo, aliyense ayenera kudziwa kuti akapanga zotsutsana ndi miyambo komanso chikhalidwe cha dera limenelo kumakhala milandu kwa amfumu.
Awa ndi mavuto akuti tikhoza kuwapewa.









