Articles
Achita zionetsero mfumu itakana kutsegula manda
- Category: Msangulutso Mzithunzi
- Published Date
- Written by Eliah Nthara
Kudali mkokemkoke masiku apitawa kwa Nyakwawa Matope ku Ndirande mumzinda wa Blantyre pomwe anthu ena adakwiya ndikuchita zionetsero pokwiya ati ndi khalidwe la nyakwayo poika patsogolo makuponi kuleka mwambo wa maliro. Anthuwo, kuphatikizapo ana asukulu yapulaimale ya Ndirande, adali kuyimba nyimbo zonyoza mfumu yawo, komanso kugenda nyumba yake, ati chifukwa adaika patsogolo kalembera wa makuponi, m’malo mokatsegula kumanda kuti akaike maliro a mwana amene adamira ndikufa m’damu la Mudi.
Malinga ndi abale a mwanayo, amene amakhala kwa Safarao ku Ndirande, mwana wawoyo adachoka ndi anzake kupita kukawedza nsomba m’damulo ndipo ataona kuti sakubwera adapita kukafufuza konse amasewera, kuphatikizapo damu la Mudi.
"Uko adapeza zovala za mwanayo zili potero ndipo anthu odziwa kusambira adayamba kufufuza mwanayo.
Atapezeka wakufa tidauza apolisi omwe adatengera thupi lake kunyumba yachisoni pa chipatala cha Gulupu," adatero mbaleyo.
Mwanayo adamira Lachisanu ndipo adapezeka Lamulungu.
Lolemba, monga mwa mwambo, a mpingo adayamba kuyendetsa mwambo wa maliro ndipo anthu adatumiza uthenga kwa Matope kuti akatsegule kumanda.
"Zinamveka kuti nyakwawayo ili kuchilinganizo chogawa makuponi ndipo siikanatha kubwera. Idangotuma nthumwi ziwiri zomwe zidabwera mochedwa kwambiri," adatero mbaleyo.
Posamvetsetsa nkhaniyo nthumwi za mfumuzo zidabwerera kwa mfumu ponena kuti anamfedwa adali kuwanyoza. Itamva izi, Nyakwawa Matope idalamula akasunge zovutazo, ndipo idaitanitsa anamfedwawo kubwalo lake.
Zovuta zitasungidwa, gulu la anthu kuphatikizapo ana a sukulu aku Ndirande Primary School komwe mwanayo ankaphunzira mu sitandade 4, anachita zionetsero zokwiya ndi khalidwe la Nyakwawa Matope, ponena kuti anayika patsogolo za makuponi kunyalanyaza maliro.
Anthuwo atachoka kumanda anapitiriza zionetserozo. Pothirirapo ndemanga, Nyakwawa Matope idati anthu okhuzidwa ndi nkhaniyi achotsedwa m’mudzi mwake. Iyo idati zomwe adachita kudali kuderera.
"Anthu amenewa achotsedwa basi. Ndinadzodzedwa ufumu m’chaka cha 1976, kodi ndi ana angati omwe atisiya kapena zovuta zingati zomwe zakhala zikugwa mudzi mwanga?" adatero Nyakwawa Matope.
Iye adavomera kuti sadapite kuzovutazo koma adatumiza nthumwi kuti zikamuyimirire kotero zimatsimikiza kuti adaliponso.
Koma mbusa Austin Malikebu wa mpingo wa Evangelical Methodist Church yemwe anayendetsa mapemphero pa maliropo adati zomwe anachita mfumu Matope nzotsutsana ndi mwambo wa Chimalawi okhudzana ndi mafumu.
"M’buku la Akorinto, Buku Lopatulika limanena kuti mfumu imatchuka ndizochita zake. Ngati mfumu ichita zoipa, imatchuka ndi zoipa, kaya anali ndi zifukwa kwa oferedwa kaya kumpingo kapena bambo wa mwana sanakaphakatikiza ku maliro. Adakayendesa za zovutazo mwa ndondomeko yake," anadandaula Malikebu.
Iye anati mwambo wa maliro umalemekeza pomwe mfumu itengapo gawo pazovuta .
Wachiwiri wofalitsa nkhani ku polisi ya Blantyre, Lameck Thembachako anati sakudziwapo kalikonse pa nkhaniyi, kotero anakana kuikira ndemanga pankhaniyi.
Koma iwo anati apolisi alibe gawo lililonse kwa maliro omwe munthu wafa yekha kaamba koti izi zimatengera miyambo ya anthu omwe akuyendetsa malirowo.
