Nation Online

Monday, May 20th

You are here: Home Every Woman Soul Malingaliro Madzi akataika

Madzi akataika

"Mayi musandiuze nzeru. Mwamunayo mumuuze kuti banja latha. Padakali pano ndaphunzira zedi. Pakufunikanso mwamuna wodziwa kuti mneni ndi mlowamalo ndi zinthu ziwiri zosiyana. Mumuuze apeze wina," adatero Patuma kuuza mayi ake atamuimbira foni.

Patuma adali mwana wa bambo ndi mayi Chaima. Iye adali ndi nzeru moti kuyambira sitandade 1 mpaka 8, ankakhala nambala 1 kapena 2 basi.

Kumbali ya chilengedwe, padalibe amene amafanana naye. Patuma adali bunthu loti likamayankhula, anyamata onse amakhala chete, kumva mawu anthetemya ngati mbalame zakumadzi.

Ndipo akamayenda, ambiri amacheuka kuti aone bwinobwino chilengedwe chimene cidamanga likulu lake kumbuyo kwake.

Atalemba mayeso ake a sitandade 8, Patuma adasankhidwa kukapitiriza maphunziro ake ku sukulu ya sekondale ya Chimweta. Nzeru zija sizidakokoloke konse ndipo mayeso ake a JCE adakhonza mochititsa manyazi ofunsa mayesowo.

Atafika Folomu 3 adapita kumsika ndi anzake kukagula zofunika kusukulu, ndipo kumeneko mkulu wina adamukakamira, kumufunsira.

Ngakhale adakana kwa nthawi, kenako adathyola khosi n’kumulola.

Sipadatenge nthawi, Patuma adapezeka kuti ali ndi pathupi pabamboyo, ndipo nthawi itakwana, adabereka mwana wamwamuna.

Tsiku lina adapita kuchipatala ndi mwana wakeyo kaamba kakutentha thupi ndipo adazizidwa nkhongono kuona kuti namwino amene adamuthandiza adali mnzake yemwe adali naye kusukulu.

Atabwerera kunyumba, adafotokozera mwamuna wake kuti akufuna kubwereranso kusukulu. Mwamunayo adali wosangalala ndi nkhaniyo poganizira kuti mtsogolo n’kudzakhala pantchito n’kumathandizana monga banja.

Patuma adayambiranso Folomu 3, pasukulu ina yoyendera. Ntchito zina za pakhomo amagwira ndi mwamunayo kuti Patuma azikhala ndi mpata wowerenga.

Mayeso a Folomu 4, Patuma adakhoza bwino zedi moti adasankhidwa kukayamba maphunziro aukachenjede.

Iye adasankhidwa kukayamba sukulu ya udotolo ndipo atamaliza maphunzirowo, adayamba ntchito pachipatala china cha boma.

Chongogwira ntchito miyei itatu, mwayi wina udamupeza kuti akaphunzire kudziko la Canada.

Adatsanzika kwa mwamuna wake, amene adamufunira zabwino zonse kokamwa inkiko.

Atafika kudziko la chilendolo, Patuma adamuimbira foni mwamunayo, kumufotokozera za momwe adayendera komanso momwe maphunziro akuyendera.

Ali kunjako, adakumananso ndi mwamuna wina amene amapitiriza maphunziro a usilikali, ndipo awiriwa adagwa m’chikondi.

Patuma adaiwala za kumudzi ndipo tsiku lina mwamuna wake ataimba foni kuchoka kumudzi, iye adamuyankha m’Chingerezi, ngakhale amadziwa kuti palibe chimene mwamuna wogulitsa matemba a Domasiyo angamve.

Adamuuziratu kuti afune wosaphunzira mnzake.

Atamaliza maphunzirowo, Patuma adabwerera kumudzi ndipo anthu onse adadabwa ndi momwe adasinthira khalidwe mwana wamkazi.

Chaka chimodzi chitadutsa, iye adakonza ukwati ndi mnyamata amene adakumana naye kunja uja, koma tsiku la ukwatilo, palibe ndi mmodzi yemwe wa kuchikazi amene adafika.

Potuluka, m’tchalitchi, mwamunayo adagwa pansi n’kukomoka. Atamutengera kuchipatala, kudapezeka kuti adali atafa kale.

Pofufuza, kudapezeka kuti mwamunayo adali atattenga masiku atatu osamwa mankhwala otalikitsa moyo, ma ARV.

Patuma adalila ngati mwana.

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh