Msungwana akufunika thandizo
- Category: Ndemanga
- Written by Nation Online
Nkhani ya msungwana wa ku Lilongwe amene sakufunanso kukhala m’mudzi yatikhudza. Poyamba, yatikhudza chifukwa msungwanayo adagwiriridwa. Kachiwiri, yatikhudza chifukwa iyeyo adaswedwanso ndi achiwembu.
Koma chimene chatikhudza kwambiri n’chakuti zikuoneka kuti msungwanayo sakulandira thandizo loyenera, zomwe zingachititse kuti mavuto ake asathe.
Apatu tikuona ngati omuzungulirawo akadapeza thandizo kuchoka ku achipatala amene akadathandiza kuti maganizo ake asapitirire kusokonekera.
Takhala tikunena kuti chipsinjo chogwiriridwa chimakhalapo mpaka kale. Choncho kumakhala kofunika kuti amene achitiridwa chipongwe chotere apatsidwe uphungu.
Kupanda kutero, mapeto ake akhoza kukhala otere.
Amene akuthandiza msungwanayu pomupatsa chakudya akuchita bwino, koma thandizo lenileni likadakhala kumutengera kuchipatala kuti adzakhale odzidalira akachira.
Â
Â








