Nation Online

Thursday, May 23rd

You are here: Home

Articles

‘Mbusa agona ndi nkhosa’ pochotsa ziwanda

 

Nkhope za nkhosa za mpingo wa Miracle International Church zinali zyolizyoli pa bwalo la milandu la Chisenjere ku Lunzu m’boma la Blantyre komwe Mbusa Jefule Leveni akuyankha mlandu womuganizira kugwiririra komanso kupereka pakati kwa mtsikana wa masiye wa zaka 17 usiku wa pa 25 Meyi ku mapemphero ochezera.

 

Koma malingana ndi woyimirira wolakwiridwa pa milandu, Christopher Daluni wa pa polisi ya Chileka wati Leveni—yemwe ali pa banja ndipo ali ndi ana atatu­—waikana nkhaniyi ku bwalo la milandu la Chisenjere.

Mkukuluzi wa nkhaniyi, malingana ndi zokambidwa pa bwalolo, ukuti Leveni, yemwe ndi wa zaka 25, akuganiziridwa kuti anagwirira mtsikanayu, wa Fomu 4, atamukopa kuti akumuchotsa ziwanda zomwe zimamuvutitsa kutulo.

Mtsikanayu wati mankhwala osiyanasiyana analephera kuthetsa vutolo ndipo anauzidwa ndi anzake kuti Leveni akhoza kulilakatitsa ndipo potsatira mapemphero akochezera linachepadi.

Daluni anati mtsikanayu, yemwe ndi wa mpingo wina, anakopeka n’kuyamba kupemphera ku Miracle International Church.

Iye anati zinthu zinatembenuka usiku wina ali kumapemphero ochezera pamene akuti mbusayu anatengera mtsikanayu kuchipinda, kumukakamiza kuti kugona naye kuthetseratu vuto lake.

"Ngakhale anamuuza kuti asaulule, zinthu zinagwa pambalambanda patadutsa miyezi itatu pamene mtsikanayu anazindikiridwa kuti ndi wodwala," anatero Daluni.

Iye anati zikalata zomwe zinaperekedwa ngati umboni pa bwalo zinasonyeza kuti chipatala cha Chileka chinakatsimikizira nkhawa za akulu omwe anakaikirapo kuti mtsikanayo anali wodwala.

Daluni anati ngakhale mbusayu anavomera pamaso pa malume a mtsikanayu kuti anachita izi ‘atayesedwa ndi demoni’, waukana mlanduwu ku bwalo la Chisenjere.

Iye anati mbusayu atazindikira kuti mtsikanayu waima, anaganiza zomutengera ku chipatala china ku Lunzu kukachotsa pathupipo.

"Mbusayu ankafuna kuchita izi ati chifukwa nkhaniyi ikadafala, omutsatira anakasiya kumukhulupirira," Daluni anatero.

Daluni anati malinga ndi umboni womwe unaperekedwa ku bwalo la mlandu, ngakhale mtsikanayu anakana kuchotsa mimbayo, munthu wa Mulunguyo anamuuzitsa kuti apemphera kuti ichoke, ndipo patatha sabata imodzi mimbayo inachokadi.

Iye anati mtsikanayu anapita ku chipatala cha Gulupu komwe anakachotsa zotsalira za mtayowo ndi kumulumikizitsa ndi apolisi a pa Chilekawa omwe anachita kafukufuku ndikutsekera m’busayu pa 17 Ogasiti 2010.

Daluni anati kalata za ku chipatala zomwe zili m’manja mwa bwalo la Chisenjere zatsimikizira za mtayowo.

Iye anati mbusayu anagona naye usiku wa pa 25 Meyi ndipo anamuuza kuti asaulule kuopa kusokoneza machiritso ndi utumiki wawo.

"Kunali ku mapemphero a m’bindikiro wa masiku atatu osala kudya ndi kupemphera komwe ndinawauza za mimba ndipo anavomera ndikundiuza kuti tipite ku chipatala china tikachotse," anatero mtsikanayu.

Azakhali a mtsikanayu omwe akumusunga ati anali wodabwa komanso wokhumudwa msungwanayo ataulula kuti pathupipo panali pa mbusayu.

"Mbusayu anatitsimikizira kuti tisakhale ndi nkhawa iliyonse chifukwa vuto la mwana wathu litha; anatiuzanso kuti tipereke chokhumba kuti mwanayu achire," anatero mayiyu akuti anapereka K1 000 m’malo mwa K5 000 yomwe mbusayo ankafuna.

"Anatiuza kuti anthu amapereka zambiri monga lamya zam’manja, K10 000 kapena ng’ombe, zomwe gulu la mbusayu limapempherera," adatero azakhaliwo.

Ndi nkhope yokwiya, bambo akunyumba kwa zakhaliyu ananenetsa kuti kuchokera pachiyambi pomwe sanamukhulupirire mbusayu.

Iye anati ngakhale banja lake linasokonekera pa nthawiyi chifukwa samagwirizana ndi mkazi wake polola msungwanayo kumapita kumapemphero ausiku.

Makolowa anati kuchokera pomwe mbusayu anasungidwa m’chitokosi cha apolisi, mkazi wake wakhala akubweretsa ndalama ndi kudzalira pakhomopo kuti akatseketse mlanduwo chifukwa iye ndi ana akuvutika.

"Ife takana kutseketsa mlanduwu, tikufuna chilungamo chioneke ndipo ena atengerepo phunziro," anatero mayi a msungwanayu.

Wotsatira Leveni, Mbusa Jemita Mchikanda, anati mpingo wawo ndi wodzadza ndi chisoni chifukwa mtsogoleriyu anasemeredwa chinyau.

Iye anati akudziwa kuti izi ndi nzeru za satana, zochokera ku mdima womwe umadana ndi kuunika, ati nz’osatheka kuti abusa awo kuchita izi.

"Abusa athu amayenda ndi atsikana ambiri; kodi iyeyu wapambana chotani kuti mpaka akawasunthe moyo? Nanga n’chifukwa chiyani anadikira kuti padutse miyezi itatu asanaulure kuti anagwiriridwa?" anadabwa Mchikanda.

Iye anati mpingo wawo ukupembedzera kuti mbusa wawo amasulidwe ndipo choonadi chioneke pa nkhaniyi.

"Loya wathu ndi Mulungu," Mchikanda anatero.

Chigamulo chili pa 2 Disembala.

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh