Nkhani
Amayi abisa katundu wa K16 000 mu panti
- Category: Nkhani
- Published Date
- Written by Bobby Kabango
Ukathyali wakasololedwe wachitika pamalo omwetsera mafuta a Puma pa Wenela pomwe apolisi adanjata mkulu wina wa ku Zambia pomuganizira kuti amathandizira amayi awiri omwe akuwaganizira kuti amatulutsa katundu mushopu pomubisa kumalo obisika.
Wakhungu apha yekha njoka ya mphiri
- Category: Nkhani
- Published Date
- Written by Steven Pembamoyo
Mnyamata wina wakhungu wagometsa anthu ku Chilinde mumzinda wa Lilongwe atakwapula mpaka kupha njoka yoopsa yomwe idalowa m’nyumba ndi kudzikulunga pamalo omwe iye amagona.
Mpingo ukana mbusa womangidwa za zitupa
- Category: Nkhani
- Published Date
- Written by Steven Pembamoyo
Mpingo wa Lord’s Chosen Charismatic Revival Ministries (LCCRM) wakana zomwe munthu wina wa ku Cameroon adauza nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno kuti iye ndi mbusa komanso mtsogolera wa mpingowu m’dziko muno.
Ng’anga ikwatira akazi 18
- Category: Nkhani
- Published Date
- Written by Gabriel Nyirenda ndi Paul Tembo
Zina ukaona kamba anga mwala, ngati munamva kuti mitala ndi nkhondo muganize kawiri chifukwa akazi 18 a sing’anga wina m’mudzi mwa Tereka kwa T/A Chikulamayembe m’boma la Rumphi atsindika kuti ndiwokhutira ndiwosangalala ndi mkuluyu.
Aphedwa kulondera chimanga
- Category: Nkhani
- Published Date
- Written by Bobby Kabango
Nyakwawa Khwalala ya kwa Senior Chief Mwadzama m’boma la Nkhotakota yaphedwa ndi achiwembu omwe amafuna kuba chimanga kumunda kwake.
Kutsatira mapazi a Chilembwe
- Category: Nkhani
- Published Date
- Written by Staff Writer
Amalawi amakumbukira mbusa John Chilembwe chifukwa cha ntchito yomwe adaigwira poyambitsa nkhondo yolimbikitsa mtundu wake kukhala woima paufulu kuchoka kunkhanza za atsamunda achizungu. Mbiri ya dziko lino imasonyeza kuti Chilembwe adayamba nkhondoyo ataba mfuti za Angerezio ku Mandala, pamalo pamene pano pali banki ya Indebank mumzinda wa Blantyre.
Mfumu ithamangitsa wobisa mwana
- Category: Nkhani
- Published Date
- Written by Steven Pembamoyo
Mfumu Simon ya m’mudzi mwa Simon kwa T/A Malili ku Lilongwe yalamula mtsikana wina Mercy Kausiwa wa zaka 22 wa m’mudzimo kuti alipire mbuzi imodzi kapena achoke m’mudzimo chifukwa chobisa mwana wa miyezi itatu m’chimbudzi poopa kuti mnyamata yemwe amafuna kumukwatira angasinthe maganizo akadziwa kuti ali ndi mwana.
‘Wakufa’ autsa mkangano
- Category: Nkhani
- Published Date
- Written by Steven Pembamoyo
Msungwana yemwe adamwalira sabata zinayi zapitazo ku Balaka wautsa mkangano pakati pa mabanja awiri atapezeka akuyendayenda mumsika wina m’bomalo.
Awiri auka kwa akufa ku Lilongwe
- Category: Nkhani
- Published Date
- Written by Steven Pembamoyo
Mavuto akukana kuwachoka mayi Nesinali Sanyadira am’mudzi mwa Kawaza kwa T/A Chiseka ku Lilongwe. Zaka ziwiri zapitazo adaona malodza ana awo awiri omwe adamwalira motsogozana atapezeka ali moyo patatha zaka 10 chiwaikireni m’manda.
Mayi wantchito apezeka atafa kuchipinda
- Category: Nkhani
- Published Date
- Written by Staff Writer
Wantchito wina wapezeka ataphedwa ndi kupachikidwa m’chipinda cha bwana wake ku Area 18B mumzinda wa Lilongwe.
Mneneri wa polisi ya Lilongwe Ramsy Mushani adatsimikiza izi ndipo adati msungwanayo, Filesi Chimombo yemwe ndi wa zaka 36 amachokera m’mudzi mwa Malanga kwa T/A Somba ku Blantyre.
Msangulutso

