Nation Online

Saturday, May 18th

You are here: Home Msangulutso Tidakumana Bwanji

Nkhani

Awiri auka kwa akufa ku Lilongwe

Mavuto akukana kuwachoka mayi Nesinali Sanyadira am’mudzi mwa Kawaza kwa T/A Chiseka ku Lilongwe. Zaka ziwiri zapitazo adaona malodza ana awo awiri omwe adamwalira motsogozana atapezeka ali moyo patatha zaka 10 chiwaikireni m’manda.

Mayi wantchito apezeka atafa kuchipinda

Wantchito wina wapezeka ataphedwa ndi kupachikidwa m’chipinda cha bwana wake ku Area 18B mumzinda wa Lilongwe.

Mneneri wa polisi ya Lilongwe Ramsy Mushani adatsimikiza izi ndipo adati msungwanayo, Filesi Chimombo yemwe ndi wa zaka 36 amachokera m’mudzi mwa Malanga kwa T/A Somba ku Blantyre.

Wakhungu apha yekha njoka ya mphiri

Mnyamata wina wakhungu wagometsa anthu ku Chilinde mumzinda wa Lilongwe atakwapula mpaka kupha njoka yoopsa yomwe idalowa m’nyumba ndi kudzikulunga pamalo omwe iye amagona.

Opopa mafuta mu transformer agwidwa

Zoti anthu ena amapopa mafuta mu transformer zimaoneka ngati nkhambakamwa. Ena amati mafuta a transformer amakaphikira tchipisi pachiwaya.

Ng’anga ikwatira akazi 18

Zina ukaona kamba anga mwala, ngati munamva kuti mitala ndi nkhondo muganize kawiri chifukwa akazi 18 a sing’anga wina m’mudzi mwa Tereka kwa T/A Chikulamayembe m’boma la Rumphi atsindika kuti ndiwokhutira ndiwosangalala ndi mkuluyu.

Gogo wodula unyolo achimina

Gogo wa zaka 75 amene adamangidwa pomuganizira kuti adadula unyolo wa munthu wina amene adathawa papolisi ya Thumbwe ku Chiradzulu wati wachimina, kumalo ozizira si kwabwino.

Mkuluyo, Jeremani Nyirenda, polankhula pafoni, adati sadzalolanso wina kumupusitsa kuchita zinthu zimene zingamulowetse m’chitokosi.

Kutsatira mapazi a Chilembwe

Amalawi amakumbukira mbusa John Chilembwe chifukwa cha ntchito yomwe adaigwira poyambitsa nkhondo yolimbikitsa mtundu wake kukhala woima paufulu kuchoka kunkhanza za atsamunda achizungu. Mbiri ya dziko lino imasonyeza kuti Chilembwe adayamba nkhondoyo ataba mfuti za Angerezio ku Mandala, pamalo pamene pano pali banki ya Indebank mumzinda wa Blantyre.

Malodza: Mwana apha mayi ake

Akale adanenadi zoona kuti m’mimba ndi m’chipala. Akadadziwa kuti wadziberekera nkhondo, mwina mayi wina ku Blantyre akadachita chotheka kuti adziteteze kuimfa m’manja mwa mwana wakeyo, koma mphuno salota anthuni!

Apolisi Lachiwiri lapitali adanjata mnyamata wa zaka 22 pomuganizira kuti adapha mayi wake wazaka 50 ku Sunnyside mumzinda wa Blantyre.

‘Wakufa’ autsa mkangano

Msungwana yemwe adamwalira sabata zinayi zapitazo ku Balaka wautsa mkangano pakati pa mabanja awiri atapezeka akuyendayenda mumsika wina m’bomalo.

Msungwana abedwa ndi a ‘Sataniki’

Msungwana wa zaka 20 ku Machinjiri mumzinda wa Blantyre akupumira mphanthi amuna ena asanu atamukakamiza kuti alowe za ‘Sataniki’ Loweruka pa 23 March.

Msungwanayu, Omega Tamulangani, wati patsikulo adauzidwa ndi mchemwali wake yemwe akukhala m’dziko la South Africa kuti apite kudepoti ya Wenela mumzindawu kukatenga katundu.