Nation Online

Sunday, May 19th

You are here: Home Religion Msangulutso Nation on Sunday Msangulutso Mzithunzi Melo wadza ndi dansi yobetcha

Melo wadza ndi dansi yobetcha

Dzina la Blessings Melo silachilendo kwa anthu okonda kumvera wailesi ya MIJ. Melo yemwe amatchukanso ndi dzina loti DJ Chivomerezi amaulutsa mapologalamu osiyanasiyana pa nyumba ya mphepoyi kuphatikizapo ija ya dansi. Martha Sande anacheza naye motere:

Tatiuza za mbiri yako.

Ndine wa chisamba m’banja la ana asanu ndipo ndinabadwa pa 19 Epulo m’chaka cha 1980 m’dziko la Zimbabwe koma kwathu ndi kwa Ngabu ku Chikhwawa. Makolo anga onse amakhala komweko moti bambo anga ndi aphunzitsi pa sukulu ya sekondale ya Makande pamene mayi anga ndi anamwino pa chipatala chaching’ono cha Ngabu.

Nanga maphunziro ako anali otani?

Ndinabwera kuchoka ku Zimbabwe ndili ndi zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ndinayamba sukulu ya pulaimale pa sukulu ya anyamata ya Fatima, kuchoka apo ndinapitirira ndi maphunziro a sekondale ku Mbiya m’boma la Nsanje. M’chaka cha 2000 ndinayamba maphunziro a utolankhani pa sukulu ya MIJ omwe ndinamaliza 2005 ndi diploma. Mwayi unandigwera chifukwa ananditenganso kuyamba kugwira ntchito monga mtolankhani ndi muulutsi pa wailesi ya sukuluyi ndikumaulutsa mapologalamu amasewero ndi dansi mwa ena.

Kodi chidwi chogwira ntchito youlutsa mau chinayamba bwanji?

Kuyambira ndili mwana ndinkasilira aulutsi monga John Phiri, Erick Knight a ku Zimbabwe. Chidwichi chinakula nditafika ku sukulu ya sekondale pomwe ndinayamba kulemba nkhani ndi kunenerera mpira wa pasukulupo. Ndipo izi zinanditakasa kukachita maphunziro a utolankhani.

Tatiuze zambiri za pulogalamu ya Dansi.

Dansi ndi pologalamu imene imasewera nyimbo zachimidzimidzi zomwe anthu kalelo ankakonda kumvera akabwera ndi Zodiak pochoka ku Sozibere. Nyimbo monga za gulu la Devera Ngwena, Leonard Dembo, John Chibadura, Sungura Boys ndi Jailos Jiri mwa ena. Pologalamuyi ndi ya kumudzi ndithu n’chifukwanso ndimadzitcha kuti mwana wa mayi Magireti.

Tatiuze za tsinde la pologalamuyi?

Nthawi zambiri pomwe ndimakhala kumudzi ndinkaona anthu akuzimitsa wailesi zawo ikakwana nthawi ya nkhomaliro kaamba ka nyimbo zachifatse zomwe zimaseweredwa m’nyumba zoulutsira mawu zambiri ndipo ndinali mmodzi mwa iwo.

Izi zinandipatsa loto lokhala ndi pologalamu yosewera nyimbo za chimidzimidzi panthawi imeneyi ndipo lotoli linakwaniritsidwa nditayamba ntchito ku wailesi ya MIJ.

Kodi ndi zovuta zotani zomwe umakumana nazo pa ntchito yako ya uulutsi ?

Ndinene apa kuti panthawi yomwe tinkatsekula malaini kuti anthu azibetcha nyimbo pa pulogalamu ya dansi kunali kovuta kulankhulana ndi wina aliyense. Motero anthu ambiri anayamba kundifunsa chifukwa chomwe sindimayankhira lamya zawo poganiza kuti ndimakondera. Izi zinandipangitsa kuyamba kutenga lamya mwa patalipatali.

Kodi zolinga zako zikukwaniritsidwa ?

Ndimasangalala chifukwa zolinga zanga zobwezeretsa chikhalidwe cha dansi ya chimidzimidzi zikukwaniritsidwa. Ndakhala ndikuona anthu ambiri m’tauni ndi kumudzi komwe akusangalala nayo pologalamuyi.

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh