Nation Online

Wednesday, May 22nd

You are here: Home Uchikumbe Kusamala chimanga: mankhwala alipo

Kusamala chimanga: mankhwala alipo

Kuumitsa bwino chimanga, kuchipeta chisanathiridwe mankhwala moyenera ndi zina mwa njira zoonetsetsa kuti chimanga chimene alimi akolola chisaonongeke ndi nankafumbwe wamkulu ngakhalenso tizirombo tina.

Malinga ndi Pulofesa Immanuel Mlenga, amene akulima ku Zomba, alimi ayenera kupeta bwino chimanga, asanachiike m’matumba. Kwa iye, mankhwala abwino otetezera chimanga ndi Alluminium Phosphate, amene akuti amathana ndi tizirombo toononga zokolola.

"Ndimaika timibuluti pakati pa matumba a chimanga ndi mtedza. Ubwino wa mankhwalawa ndi wakuti, sikuti umachita kuthira chimangacho, zomwe zimachititsanso kuti chisaononge umoyo wa amene akuchidya. Pakatha miyezi itatu, timachotsa mankhwalawo," adatero Mlenga.

Iye adati akatero amakutira chimangacho ndi pulasitiki.

Malinga ndi iye, kupeta bwino chimanga chisanaikidwe m’matumba kumathandiza kuti nthawi yomwe alimi akufuna kupita kuchigayo adzangotenga chimangacho, osavutikanso ndi kupeta kachiwiri.

Matumba abwino

Mlembi wamkulu muunduna wa malimidwe Erica Maganga adati alimi aonetsetse kuti matumba ndi a ukhondo.

"Ngati akugwiritsanso ntchito kuchokera chaka chatha, awawiritse kaye kuti tizirombo ndi mazira ake tife. Chimanga choikidwa m’matumba chiyenera kukhala chouma bwino komanso chomwe chathiridwa mankhwala woyenera pa mlingo woyenera," adatero Maganga.

Kwa amene akuika chimanga m’nkhokwe, Maganga adati ayenera kutonola chimangacho poopetsa nankafumbwe wamkulu. Nankafumbweyu amakonda chimanga cha kuchitsononkho.

"Alimi aonetsetsenso kuti nkhokwe zawo zatetezedwa kuzirombo zoononga zokolola," adatero Maganga.

Malinga ndi mmodzi mwa akuluakulu a ku nthambi ya mankhwala ophera tizirombo ya Petsicide Control Board Rhodrick Ndawala adati alimi ayenera kuthira mankhwala ovomerezeka monga Actellic Super, Shumba Super, Spintor Dust, Chikala Super komanso Phostixin.

Mankhwala oyenera

Ambiri mwa mankhwalawa ndi a ufa, ndipo Ndawala adati alimi ayenera kuthira mankhwalawa ku chimanga chimene chaikidwa papepala la pulasitiki.

"Mlingo woyenera ndi kudzadzitsa zibiriti ziwiri za mankhwala n’kuthira ku chimanga cholemera makilogalamu 50. Chimangacho akhozanso kuchiika pa lona, mphasa kapena mkeka," adatero Ndawala.

Iye adati mankhwala a madzi monga Actellic Super 50% kapena Superguard 50%, alimi atenge mamililita 20 ku lita imodzi ya madzi ndipo athire kumatumba 20 olemera makilogalamu 50 lililonse.

Ndawala adatinso mankhwala ophera tizirombo ena monga Seven sayenera kuthiridwa kuzokolola chifukwa amadzetsa mavuto ena m’thupi.

"Mankhwala alionse ali ndi mlingo wake, komanso alimi akumbuke kuti sibwino kuthira mankhwala lero mawa kukagaitsa. Ndibwino kuti padutse miyezi itatu chimanga asanachigaitse kapena kuchidya akathira mankhwala," adatero Ndawala.

Malinga ndi unduna wa malimidwe, nankafumbwe wamkulu ndi chimodzi mwa tizirombo tosautsa timene timachititsa kuti makilogalamu 12 ndi theka pa 100 alionse amene alimi akolola azionongeka.

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh