Nation Online

Monday, May 20th

You are here: Home Uchikumbe Makwacha osaneneka mu bowa

Makwacha osaneneka mu bowa

Katswiri wa bowa kusukulu ya ukachenjede ya Bunda College Vincent Mwale wati muulimiwu muli phindu la mnanu koma anthu ambiri sakudziwa izi.

Polankhula ndi Uchikumbe m’sabatayi, Mwale adati n’zokhumudwitsa kuti bowa sukulimidwa mokwanira.

"Ndizomvetsa chisoni kuti ngakhale bowa uli ndi phindu loposa, alimi ambiri sanazindikirebe za izi. Komatu bowa muli chuma chochuluka," adatero Mwale.

Iye wafotokoza kuti padakali pano bowa akugulitsidwa pa mtengo wa pakati pa K 500 ndi K1 500 pakilogalamu ndipo msika ulipo wokwanila kamba koti ichi ndi chakudya ndipo anthu amachifuna nthawi zonse.

"Mwachitsanzo, anthu omwe ali ndi nyumba zodyeramo anthu, akumagula bowa wochuluka, komanso anthu paokha m’makukamu akugula kwambiri bowa," adatero Mwale.

Padakali pano Bunda College ikugwira ntchito ndi ena mwa alimi ang’onoang’ono omwe adaonetsa chidwi pa ulimiwu. Awa ndi monga alimi a gulu la Chalela ku Mitundu, ku Mzimba, Balaka ngakhalenso ku Blantyre.

"Ngakhale izi zili chomwecho palinso mwayi woti alimi atha kukagulitsa bowayu m’mahotela. Koma vuto ndi lakuti pakadali pano palibe alimi akuluakulu omwe angathe kudzithemba kuti angakagulitse ku mahotelawa. Izi zikupangitsa kuti titaye mwayi wa msika," adaonjezera Mwale.

Bowa ndi mbewu yomwe siilira zambiri pobzala, chifukwa imatha kubzalidwa pa mapesi komanso ka malo kochepa kwambiri koma ndi kukolola zambili.

"Ndipo mbewuyi imachita bwino chaka chonse. Bowa amatakasuka ngakhale nyengo yozizira kapena yotentha," adatero katswiriyo.

Mwale adatinso mbewuyi imatha kugwira bwino m’maboma onse adziko lino kotero kuti dziko lino lili ndi mwayi wawukulu wopha makwacha kuchokera ku mbewu.

Ena mwa mavuto pa ulimi wa mbewuyi ndi woti anthu ambiri alibe luso kapena kuti ukadaulo wa momwe angalimire mbewuyi. Komanso ena sadziwa za nkhani ya misika.

Mwale adati: "Padakali pano, Bunda College ikuphunzitsa alangizi a zaulimi za momwe angatukulile ulimiwu."

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh