Nkhani

‘Kachali asayang’anire Bungwe la zisankho’

Bungwe lounikira za ufulu wa Amalawi komanso mgwirizano wa mabungwe pa zisankho adzudzula mtsogoleri wa dziko lino posankha wachiwiri wake Khumbo Kachali kukhala mkulu yoyang’anira bungwe la zisankho la Electoral Commission (EC).

Mabungwe a Malawi Watch ndi Malawi Electoral Support Network (Mesn) ati uku n’kuika khoswe pamkhate chifukwa Kachali ndi chipani chake cha PP adzapikisana nawo pachisankho cha 2014 chomwe a EC akuyendetsa.

Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wachibadwidwe la Malawi Watch, Billy Banda, kudzanso mneneri wa bungwe lowona za zisankho la Malawi Electoral Support Network (Mesn), Steven Duwa, ati ngati Banda sasintha ganizoli ndiye kuti iwo sadzapita kuchisankho cha 2014 chifukwa izi ndi zokonza kale.

Zitangodziwika kuti Pulezidenti Joyce Banda wasankha wachiwiri wake kuti asenze udindo woyang’anira bungweli, bungwe la European Union (EU) lidachititsa mtsutso pankhani ya ufulu wachibadwidwe ndipo pamtsutsowo mkulu wa EC, Maxon Mbendera, adadabwanso ndi ganizo la boma kotero wafunsa mlangizi wa mtsogoleri wa dziko lino pa malamulo, Anthony Kamanga, kuti awafotokozere momwe agwirire ntchito ndi Kachali.

Ndime 76 (4) ya malamulo oyendetsera dziko lino imati: “Pogwira ntchito kapena kuyendetsa udindo wawo malinga ndi ndime ino bungwe loyendetsa chisankho silizikakamizidwa kapena kuopsezedwa ndi munthu aliyense.”

Apa Billy Banda adati zomwe wachita mtsogoleriyu poswa malamulo a dziko lino atha kutengeredwa kubwalo la milandu chifukwa malamulowo si a munthu mmodzi. “Zachitikazi ndi zosakomera Amalawi ndipo Amalawi salola zimenezi. Akumbukire bwino kuti m’boma la DPP Amalawi adakwiya pomwe Bingu wa Mutharika adatseka bungwelo.

“Zikuonetseratu kuti mtsogoleriyu ali ndi zolinga zolakwika chifukwa sakutsatsa malamulo. Khumbo Kachali, yemwe amusankhayo, akufunanso atadzaimira nawo m’masankho ndiye zingatheke kuti nayenso akhale pamphika?” akufunsa Banda.

Iye wati ngati izi sizisinthidwa, bungwelo limema Amalawi kuti achite zionetsero posonyeza kukwiya kwawo komanso kuti asadzavote.

Mogwirizana ndi Banda, Duwa wati wakwiya ndi ganizoli chifukwa bungwelo limayenera ligwire ntchito modziimira palokha.

Iye wati bungwe lawo lalembera kalata mtsogoleriyu kuti asinthe ganizo lake.

“Timenya nkhondo mpaka izi zisinthidwe. Ngati sabweza ganizo lawo ndiye sitidzavota,” adatero Duwa.

Koma mneneri wa boma, Moses Kunkuyu, yemwenso ndi nduna yofalitsa nkhani, wati palibe chachinyengo chilichonse chomwe chingachitike chifukwa Kachali sagwira ntchito ku EC.

“Udindo umene wachiwiri kwa Pulezidenti wapatsidwa sikukhudzana ndi chilichonse cha chisankho. Iwo ali pakhomo poti ngati a EC akufuna thandizo ndi zina zoyendetsera zisankho azikapeza wachiwiri kwa Pulezidenti.

“Udindowu udali m’manja mwa a Pulezidenti ndiye iwo awupereka kwa wachiwiri wawo. Amabungwe ngati sakumvetsa afunse, si bwino kumangolankhula kuti achoke pampando chikhalirecho sadamvetse chomwe chachitika,” adatero Kunkuyu.

Kachali wakhala akudzudzulidwa ndi amabungwe komanso Amalawi kuti samalankhula bwino ndipo akuyenera kuchotsedwa pa mpando wa wachiwiri kwa pulezidenti.

Potsegulira chipatala ku Lupaso m’boma la Karonga, iye adadzudzula anthu omwe amadzudzula iye ndi Pulezidenti Banda kuti akuyendayenda kwambiri ponena kuti ‘samayenda m’makomo mwa amanu kapena abambo anu.’

Kachali adakhudzidwanso ndi nkhani yosowetsedwa kwa mabedi 13 omwe adatengedwa pachipatala cha Mponera ndi kuwapititsa ku Mzimba komwe panthawiyo kumachitika zisankho zapadera za aphungu a ku Nyumba ya Malamulo.

Kaamba zimenezi, Amalawi ambiri akukaika ngati Kachali ndi munthu woti angamudalire kuti akhoza kuyendetsa zinthu mokomera Amalawi onse mosakondera.

Malinga ndi Billy Banda, kaamba ka zomwe Kachali adachita, sikungakhale kulondola kumupatsa udindo ngati umenewu chifukwa Amalawi sangamukhulupirirenso.

Related Articles

Back to top button