Nkhani

182 adzipha mu sept

Listen to this article

Chiwerengero cha anthu omwe akudzipha chikunka chikwera m’dziko muno. Kafukufuku amene Msangulutso adapanga akuonetsa kuti sipakutha sabata osamva nkhani kuti wina wadzipha ndipo ambiri mwa anthuwa akudzipha kaamba ka mavuto a za chuma makamaka ntchito ikatha kapena ngongole zikafika m’nkhosi, kumwa mowa mwauchidakwa, kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo komanso mavuto a maubwenzi ngakhalenso a m’banja.

Izitu zimadzetsa matenda a nkhawa ndipo pamapeto pa zonse ngati salandira thandizo pa nthawi yake, amadzipha.

Mchitidwe wodzipha ukuchulukira

Mwachitsanzo, m’sabata yapitayi bambo wina wa zaka 52, Simplex Phiri adadzikhweza atamuimika kuntchito komwe amagwira ku Mwimba m’boma la Kasungu.

Malinga ndi malipoti apolisi, pofika Lachitatu, anthu 182 adzipha kale mwezi uno poyerekeza ndi anthu 119 pa nthawi yomwyi, chaka chatha.

Chiwerengeroch tikachigawa chikuonetsa kuti mwa anthuwa,  111 adzipha kuchokera m’chigawo cha pakati, pomwe chaka chatha adali 61.

Ndipo anthu 51, adzipha m’chigawo cha kumpoto, poyerekeza ndi 42 omwe adadzipha chaka chatha.

Pomwe anthu 15 adadzipha pogwiritsa ntchto njira zosiyansiyana m’chigawo cha kumwera poyerekeza ndi anthu 10 chaka chatha ndipo kuchigawo cha ku m’mawa, anthu 5 ndiwo adzipha poyerekeza ndi anthu atatu chaka chatha.

Wachiwiri kwa mneneri wapolisi m’dziko muno Peter Kalaya adati chiwerengerochi chakwera ndi 57 mwa 100 alionse.

“Mwa anthuwa, akuchulukira ndi amuna kuposa amayi,” adalongosola Kalaya.

Polankhulapo, mkulu wa bungwe la St John of God lomwe limaphunzitsa adotolo a matenda a nkhawa komanso limasamala anthu odwala matendawa, Charles Masulani adati chiwerengerochi chakhala chikukwera kwa zaka ziwiri zapitazo.

Malinga ndi Masulani, kafukufuku yemwe adachita m’chaka cha 2018 adaonetsa kuti anthu 9 amadzipha mwa anthu 100 000 alionse.

“M’kafukufuku wathu tidapeza kuti anthu ambiri akudzipha maubale kapena maubwenzi awo akasokonekera, nkhani za chuma zikavuta komanso kusakhulupilirana m’banja,” Masulani adalongosola.

Ndipo iye adati komanso anthu ena akumwa mowa ndi kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo moonjeza mpaka kudzipha nawo.

Kafukufuku wa bungwelo adaonetsa kuti gwero lodzipha ndi matenda a m’maganizo ndipo n’kofunika kuti anthu adziwe zambiri za matendawa.

“Munthu akabwera kuchipatala kuno ndi matenda amenewa, timamugoneka ndipo amakhala ndi namwino nthawi iliyonse. Akakhazikika ndi pomwe amalandira uphungu,” adalongosola Masulani.

Iye adatinso abambo ambiri akudzipha chifukwa sagawana nkhawa zawo ndi anthu ena ndipo pamapeto pa zonse zimawalemera pomwe amayi amapeza thandizo akakhala ndi nkhawa.

Masulani adatinso mpofunika kuunikanso malamulo a dziko lino omwe amanjata munthu akakhala ndi malingaliro ofuna kudzipha.

“Anthu amaopa kudzalandira thandizo poganiza kuti apolisi akangodziwa kuti akufuna kudzipha, awanjata choncho boma lichotse lamuloli kuti anthu azilandira thandizo momasuka,” adatero Masulani.

Iye adati anthu enanso amaopa kulandira thandizo akakhala ndi maganizo ofuna kudzipha chifukwa cha zikhulupiriro zomwe zimati kudzipha kumayenda m’magazi a kumtundu komanso munthu akadzipha ndiye kuti wakhwimiridwa.

“Komatu choti anthu adziwe n’choti munthu kufika podzipha amakhala kuti wasunga vuto ndipo ngati pamathero pokoka mphira, nawo ubongo wake wafika pamathero. Anthuwa akufunika kusaka thandizo ku chipatala, ngakhale kumipingo, aphungu a m’midzi komanso aliyense yemwe akumukhulupilira,” Masulani adamaliza motero.

Related Articles

Back to top button