Chichewa

2017 yatilandira ndi zigumula

Listen to this article

 

Pangotha sabata chilowereni chaka cha 2017, koma malipoti a ngozi zakudza ndi mvula m’maboma osiyanasiyana atopetsa kale.

Nyumba, sukulu, misewu, katundu ndi zakudya za anthu ena zaonongeka ndipo Amalawi ena ali pamavuto kaamba ka ngozizo.

Lachitatu lapitali, nyumba 32 zidasasuka kudzanso zipupa zina kugwa kaamba ka mvula ya mphepo ya mkuntho yomwe idagwa kwa mfumu yaikulu Mkukula m’boma la Dowa komwe idaononga katundu ndi chakudya.

Mlatho wa pa Jalawe ku Rumphi udaguvukira mvula itakokolola zoulimbitsa

Agulupu aakulu a Mengwe omwe dera lawo lidakhudzidwa kwambiri adati mvula ndi mphepozo zidayamba m’ma 3 Koloko masana a tsikulo ndipo m’mudzimo mudali kokakoka anthu kusowa kolowera ndi pogwira.

“Chakudya chathu monga ufa, pogona ndi zofunda komanso katundu wina ofunika zidaonongeka pangoziyo moti ndi mwayi kuti palibe yemwe adavulala,” adatero Mengwe.

Mkulu wapolisi m’bomalo Felix Phiri adakafotokozera ofesi ya DC momwe zinthu zilili apolisi atakayendera madera okhudzidwawo kuti athandizane zochita.

Lachitatu lomwelo, anthu 7 adavulala pamalo okwerera basi a Mibawa mumzinda wa Blantyre mvula yamphamvu itazula chimtengo chomwe chidali pafupi ndi malowo nkuwugwetsera pa maminibasi 7.

Lachiwiri, mvula ina ya mphamvu idakokolola mlatho wa Jalawe omwe umalumikiza maboma a Rumphi ndi Karonga pa msewu wa M1.

Malingana ndi DC wa m’boma la Rumphi Lusizi Nhlane, mvula yamphamvu idagwa usiku wa Lachiwiri zomwe zidapangitsa kuti madzi aziyenda mwamphamvu mpakana kufowola mizati ya mlathowo omwe udakokoloka.

Ngozi zina zokhudzana ndi mvula yamkuntho zidachitika tsiku loyembekeza kulandira chaka cha tsopano pa 31 December, 2016 m’dera la mfumu yaikulu Nanseta m’boma la Thyolo komwe nyumba 114 zidaonongeka.

Kauni yemwe khonsolo ya boma la Thyolo adachita wasonyeza kuti chiyambire mvula ya chaka chino, nyumba 1 000 ndizo zakhudzidwa ndipo izi zapangitsa kuti mavuto a malo okhalapo akule m’bomali.

Pa 31 December, 2016 pomwepo, nyumba 96 zidaonongeka ndi mvula yamkuntho yomwe idagwa m’boma la Karonga ndipo a komiti ya zachitetezo ya District Civil Protection (DCPC) adati izi zidafikitsa chiwerengero cha nyumba zokhudzidwa pa 424 m’bomali.

Komitiyo idati midzi ya Mwamutawali, Mponera ndi Mwandovi ndi ina mwa midzi yomwe yakhudzidwa ndi mvula zolusazi m’bomali ndipo zina mwa zomwe zaonongekeratu ndi sukulu ya pulaimale ya Chisumbu ndi msika wa Jetty.

Nthambi yoona zanyengo m’dziko muno idalengeza kumayambiriro a Mvula kuti chaka chino dziko lino liyembekezere mvula yamkuntho chifukwa cha mphepo ya La Nina yomwe nthawi zambiri imabweretsa mvula yamtunduwu.

Pankhaniyi, mneneri wa nthambi yoona ngozi za dzidzidzi Jeremiah Mphande adati ndilokonzeka kulimbana ndi zotsatira za Mvula ya mtunduwu itati yabwera chifukwa ilo mothandizana ndi maiko ena komanso mabungwe adakhazikitsa kale ndondomeko zoyenera.

“Kumbali yopulumutsa anthu ngozi yotere itachitika, tili bwino kale chifukwa anthu odzagwira ntchito imeneyi adaphunzira kale ndipo nthawi iliyonse tikhala tikuwatumiza mmaboma ndi m’madera momwe ngozizi zimachitika kawirikawiri,” adatero Mphande. n

Related Articles

Back to top button
Translate »