Nkhani

‘Kunjatidwa kwa Kasambara kunganyanyule mavuto’

Kusamvera mabwalo a milandu komwe boma laonetsa kwasonyeza kulephera kwa chipani cha Democratic Progressive (DPP) pa kulemekeza ufulu wachibadwe, zomwe ati zingakhale ndi zotsatira zoipa.

Azipani zotsutsa boma, amabungwe oona za ufulu wachibadwidwe, mfumu ina kudzanso anthu m’madera osiyanasiyana aunikira izi pomwe apolisi adakakamira kusunga mmodzi mwa akatswiri woimira anthu pamilandu, chonsecho bwalo lamilandu litampatsa belo.

Ralph Kasambara-yemwe wakhala akudzudzula boma m’zambiri komanso kuimira pamilandu odzudzula boma-adamangidwa Lolemba pa 13 Febuluwale poganiziridwa kuvulaza anthu omwe ati amafuna kumupha komanso kuphulitsa nyumba yake ndi bomba la petulo.

Ngakhale womuimira pamilandu adatenga belo ya bwalo lamilandu kuti Kasambara atulutsidwe, apolisi sadamulole kutuluka, kufikira Lachiwiri pa 21 Febuluwale pomwe adatulutsidwa pa belo.

Apa omwe aikirapo ndemanga ati izi zingapereke chithunzithunzi choti boma silikulabadira za ufulu wachibadwidwe ndipo likutseka pakamwa Amalawi otsutsana ndi ulamuliro wa DPP komanso mtsogoleri wa dziko lino, Bingu wa Mutharika.

Ndemangazi zati mwa zina maiko ndi mabungwe akunja angapitirize kumana dziko lino thandizo chifukwa boma silikulemekeza ufulu wachibadwidwe.

Dziwani Tuwanje wa m’mudzi mwa Chiwalo kwa T/A Chiwalo ku Phalombe wati izi zikungosonyeza kuti ufulu wobadwa nawo uli pachiopsezo.

“Ife timadalira anthu omenyera ufulu ngati amenewa; ngati akumangidwa pazifukwa zonsamveka bwino ndiye kuti ifenso tili pachiopsezo,” akutero Tuwanje.

Samuel Luangwa wa m’mudzi mwa Maulabo kwa T/A Maulabo m’boma la Mzimba wati moyo wa anthu uli pachiwopsezo, maka ngati zizifika pokanzidwa belo chonsecho bwalo lamilandu litaloleza.

Mfumu ina yaikulu ku Mwanza yomwe siidafune kutchulidwa dzina yati sikumvetsa chomwe Kasambara amakaniziridwa belo.

“Monga mfumu, ndikuti ndikulakwa kukaniza Kasambara kutuluka pa belo. Ufulu wathu uli pachiopsezo chachikulu.

“Apa boma likuchita kuonetseratu nkhanza zonse. Izi zikutipatsa uthenga woipa kumudzi kuno kuti ngati ena atalankhula zosakhala bwino ndiye kuti azingomutumizira anthu achipani ndikumukhapa, mwina kumuotchera nyumba kumene,” ikutero mfumuyi.

Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wachibadwidwe la Malawi Watch, Billy Banda wati mawanga aboma pankhani ya Kasambara akuonetsa kuti boma la DPP silikuimira mzika za Malawi chifukwa likapemphedwa kuti likonze likuganiza kuti akunenayo akufuna kulanda boma.

“Maiko akunja akhoza kudula thandizo dziko chifukwa chilichonse chikuchitika mokomera munthu mmodzi,” akutero Banda.

Mtsogoleri wachipani cha Petra, Kamuzu Chibambo, wati maso a dziko akuyenera kumakhala kwa anthu a kumudzi chifukwa amazunzika ngati awanenera zamavuto awo alibe mwayi odzudzula boma.

Iye adanenetsa kuti anthu akumudzi asadandaule kwambiri pa nkhani ya Kasambara chifukwa azipani ayesetsa kuti chilungamo chioneke.

Kasambara-yemwe kale adali mlangizi woyambirira wa boma pazamalamulo m’boma la Bingu wa Mutharika-wakhala akudzudzula boma pa zokhudza ulamuliro wabwino.

Iye damangidwa pamodzi ndi Arthur Chikankheni, Mayamiko Kadango, Brian Magoya, Patrick Gadama ndi Ali Kaka ndipo adatulutsidwa pa belo ya bwalo lamilandu Lachitatu pa 15.

Koma mwa onsewa, Kasambara yekha adamangidwanso patangotha maola awiri, ati ndondomeko zotulutsira amunawa sizidatsatidwe.

Koma mneneri wa mtsogoleri wa dziko lino, Hetherwick Ntaba, wati anthuwa akuyenera kumvetsa nkhanza zomwe adachita Kasambara pootcha anthu osalakwa kumaliseche ndi moto wa magetsi, uko atawamanga.

Iye wati izi sindale ndipo palibe chisonyezo chilichonse kuti boma lachipani cha DPP lasiya kulemekeza ufulu wachibadwidwe.

Lachinayi pa 16 Febuluwale, Kasambara adatengeredwa ku ndende ya Zomba komwe adasungidwa pamodzi ndi akaidi wodikira kuphedwa kapena kuseweza moyo wawo wonse.

Lachisanu, Kasambara adamutengera kuchipatala cha Mwaiwathu mumzinda wa Blantyre kuti akalandire chithandizo chachipatala, ati malinga ndi vuto lake la mtima.

Koma Ntaba wati mwina anthu sakumvetsetsa, ati apolisi sangangomanga munthu popanda chifukwa.

“Nokha mwamva kuti belo yomwe adapatsidwa idali yosasayinidwa ndi apolisi ndiye kumumanganso sikuti pali zifukwa za ndale apa.

“Kasambara wakhala akulankhula chipongwe m’mbuyo monsemu koma bwanji samamangidwa ngati zili zifukwa za ndale?” akutero Ntaba.

Malinga woimira Kasambara pamilandu, Wapona Kita, ngakhale Kasambara watulutsidwa pa belo sizikudziwika kuti adzikaonekera masiku ati.

Pomwe timasindikiza nkhaniyi n’kuti Kasambara ali kuchipatala cha Mwaiwathu mumzinda wa Blantyre, kuyembekezera kupita kunja ku chipatala Lachinayi.

Related Articles

Back to top button