Nkhani

‘Aphungu apite m’midzi’

Pomwe sipikala wa nyumba ya malamulo, Henry Chimunthu Banda walengeza Lachitatu m’sabatayi kuti aphungu ayamba kukumana pa 18 Meyi, T/A Mwakaboko ya m’boma la Karonga yati aphunguwa akuyenera apite kumudzi kukamva zomwe anthu awo akufuna kuti akakambirane.

Mfumuyi yati aphunguwa amangonama kuti zomwe akukambiranazo zikuchoka kwa anthu omwe adawasankha chikhalirecho samapitako.

Mwakaboko wati aphungu akumakhala m’tauni zomwe zikulepheretsa kuti mbalizi zizikambirana zosowekera za dera lawo.

Mfumuyi yati ikhala yokondwa kuti pakhale yankho la mavuto a kusowa kwa mafuta agalimoto.

Mwakaboko watinso njira yosankhira ophunzira opita kusukulu ya ukachenjede ikuyeneranso kukambidwa.

“Mukumbuka bwino kuti kuno takhala tikudandaula ndi ndondomokoyi ndiye ndibwino aphunguwo akakambirane zimenezi,” adatero Mwakaboko.

William Joseph wa m’mudzi mwa Goveya kwa T/A Makwangwala ku Ntcheu wati pa 18 pasadafike aphunguwa apite kumudzi kukafunsa osati kumangowaimbira lamya pazomwe akakambirane.

Mlimi wa chimangayu wati ndibwinonso kuti aphunguwa akakambirane

zochotsa ndondomeko yosadalira chithandizo chakunja ya Zero-deficit.

Iye wati anthu avutika kwambiri maka pokwera misonkho kwa zinthu chifukwa cha ndondomekoyo.

Related Articles

Back to top button