Nkhani

‘Bajeti sidaganizire anthu akumudzi’

Listen to this article

 

Ali ndi mwana agwiritse, akutero amabungwe ati poti ndondomeko ya boma ya chuma ya chaka cha 2012 mpaka 2013 inayenera kulingalira bwino zochepetsera munthu wakumudzi ululu wa kugwa kwa ndalama ya kwacha.

Izi aunikira ndi mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (Cama), John Kapito, mphunzitsi wa zachuma ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Ben Kaluwa, mafumu ndi anthu ena m’sabatayi.

Apa n’kuti aphungu ena ku Nyumba ya Malamulo atandaulanso ndi ndondomekoyi pomwe inaperekedwa ndi nduna ya zachuma, Dr Ken Lipenga, m’nyumbayo Lachisanu sabata yatha kuti aphungu ayambe kukambirana.

Ndemangazi zalunjika poti ndondomekoyi ikomere akumudzi omwe achulukira malinga ndi kalembera wa anthu wa 2008.

Kalemberayo adaloleza kuti chiwerengero cha anthu m’dziko muno chili pafupifupi 13 miliyoni.

Mwa chiwerengerochi, pafupifupi anthu 84 mwa 100 alionse amakhala kumudzi ndipo 16 otsalawo ndi amene ali m’matauni ndi m’mizinda.

Mavuto akulu

Kapito wati malinga ndikugwa kwa ndalama ya kwacha, moyo wa anthu akumudzi uli pamoto.

“Boma lachotsa msonkho pa nyuzipepala, buledi ndi kaunjika koma mutha kuwona kuti izi ndi za anthu a m’tawuni mokha, osati a kumudzi.

“Njira yopulumutsira munthu wakumudzi ndi kumupatsa maganyu opezerapo kangachepe,” watero Kapito.

Iye watinso boma likuyenera kukhazikitsa njira zoti katundu kumudzi asamakwere moboola m’thumba.

Kaluwa wati boma langoika chidwi pa anthu a m’mizinda ndi m’matauni ndipo n’koyenera lichitepo kanthu pa madandaulowo a akumudzi.

“Mbali ya zamaphunziro ndi ya zipangizo zotsika mtengo ndikomwe ndikuona ngati ndondomekoyi yaserapo kuthandiza wakumudzi.

Lolemba lathali, aphungu a ku Nyumba ya Malamulo adapemphanso boma kuti likhazikitse njira zothandizira anthu a kumudzi.

Mneneri wa zachuma kuchipani cha MCP, Joseph Njobvuyalema, anati boma laika patsogolo munthu wa mtauni, osati wakumudzi.

Zipangizo zaulele

Njobvuyalema wati boma lidakaonetsetsa kuti ndondomekoyo ikupatsa munthu wakumudzi ntchito kapena ganyu kuti atha kupeza ndalama.

“Kugwa kwa ndalama ya kwacha ndi pafupifupi ndi theka la mphamvu zake ndi vuto lalikulu kwa munthu wakumudzi chifukwa zinthu zidakwera pomwe iye alibe pogwira,” adatero Njobvuyalema.

T/A Phambala ya m’boma la Ntcheu yati ngakhale ndondomekoyi ya chaka chino yaikabe ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo, komabe wati boma lichite kanthu pofewetsa moyo wa munthu wakumudzi.

Iye wati boma likuyenera lipitirize ndondomeko ya nthandizi yomwe akuti ndiyo ingapindulire anthu akumudzi.

“Otenga nawo mbali pantchito za pansi pa ndondomeko ya nthandizi amalipidwa pomwe agwira ntchito. Patsiku amalandira amalandira K200.

“Boma liganizire zobweretsanso ndondomekoyi komanso kukweza malipiro kufika pa K400,” watero Phambala.

Mfumu Yaikulu Themba Chikulamayembe ya m’boma la Rumphi yati kumudziko zinthu zakwera mtengo kotero boma liike njira zoti anthu akumudzi athandizike.

Bajeti isinthe miyoyo

Mary Jimu wa m’boma la Chikhwawa kwa T/A Mulolo wati anthu akumudziko avutika chifukwa ndondomekoyi sidasinthe moyo wawo.

“Tili ndi mabungwe kumudzi kuno, bwenzi boma litaika ndalama m’mabungwemo kuti azithandizira anthu akumudzi kuno.

“Titha kumapeza ngongole kapena ntchito zakumudzi. Koma momwe zilili moyo ukhala wovutirako,” adatero Jimu.

Thoko Loga yemwe amathira utoto galimoto ku Chilinde mumzinda wa Blantyre wati m’ndondomeko ya zachumayo mulibe chawo.

“Ntchito zikusowa. Maso a boma akhale pa anthu omwe saali pantchito chifukwa zinthu zakwera mtengo. Yemwe sakugwira ntchito akugulabe zinthuzo pa mtengo wokwerawo,” adatero Loga.

Koma Mneneri wa boma, Moses Kunkuyu, wati ndondomekoyi yayesetsa kufungatira akumudzi. Iye watinso anthu asaiwale kuti ndondomekoyi ya chaka chinoyi ndi yofuna kukonza chuma chomwe pakatipa sichimayenda bwino.

Iye wati m’ndondomekoyi muli zina zomwe zingapindulire munthu wakumudzi monga ndalama zomwe zalowa m’gawo la chitukuko cha kumudzi ya Social Cash Transfer.

“Tikati kukonzanso sikutanthauza kuti mukukonza mtauni mokha ndikusiya kumudzi. Zilipo zambiri zopindulira munthu wakumudzi.

“Mwachitsanzo, kuchotsa misonkho pa buledi ndi zina zipindulira munthu wakumudzi,” adatero Kunkuyu.

Anthu enanso anayamikira kale ndondomeko ya chaka chino yomwe ndi ya K406 biliyoni kusiyana ndi ya chaka chatha ya K394 biliyoni.

Unduna wa zamaphunziro walandira K74 biliyoni yomwe ndi yochuluka kuponsa maunduna ena onse.

Chaka chatha undunawo unali ndi K54 biliyoni.

Unduna wa zaulimi walandira K68 biliyoni yomwe K40 biliyoni ndi ya zipangizo zotsika mtengo.

Related Articles

Back to top button