Nkhani

‘Bingu adafa bwanji, pakhale kafukufuku’

Listen to this article

A mabungwe omwe si a boma, mfumu ina yaikulu komanso anthu angapo otumikiridwa ati n’koyenera kuti Amalawi adziwe bwino lomwe za imfa ya mtsogoleri wakale wa dziko lino Bingu wa Mutharika choncho boma lisagonjere malingaliro ojejemetsa kafukufuku pankhaniyo.

Kuunikiraku kwadza pomwe boma ndi banja la Mutharika akhala akuponyerana Chichewa pa ganizo la kafukufuku pa imfayo.

Pomwe a boma komanso mtsogoleri wa dziko lino Mayi Joyce Banda akhala akutsindika kufunika kwa zofufuzazo, akubanja malemuyo akhala akuti n’kosayenera kutero chifukwa ati chomwe chidapha wawo chidadziwika kale.

Koma m’sabatayi ndemanga zati Mutharika anali wotumikira dziko, osati banja lokha, kotero anthu ayenera amve mvemvemve dziwe zambiri pa imfa ya mtsogoleriyo.

Mutharika adamwalira ndi matenda a mtima adzidzidzi ku mayambiliro a Epulo ndipo adalowa m’manda pa 23 Epulo.

Mwa zina, chinsinsi chachikulu chidakuta nkhani ya matenda komanso imfayo.

Malipoti a maudindo angapo amatsutsana; ena kumati Mutharika adamwalirira ku chipatala cha Kamuzu Central, ena amati kunyumba ya boma ku Lilongwe ndipo enanso amati ku chipatala m’dziko la South Africa.

Pamtanda wa Bingu

Nazo zolembedwa pa mtanda wosonyeza tsiku lobadwa komanso la kumwalira kwa Mutharika zimasinthasintha; mtanda wina umati anamwalira pa 5 Epulo, wina pa 6 Epulo ndipo wina n’kumati pa 7 Epulo.

Masiku awiri thupi la Mutharika lisadalowe m’manda, ofesi ya Pulezidenti ndi nduna zake idati malemuyo adamwalira pa 5 Epulo koma mtanda womaliza udasonyeza kuti iye adatisiya pa 6 Epulo.

Apa anthu akhala akuti tsopano n’koyenera kudziwa tsiku lenileni lomwe Mutharika adamwalira komanso tsatanetsatane wa nthawi, malo komanso zochitika zomwe zidazinga maola ake omaliza.

 Pa 4 Juni 2012, mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda, adalumbiritsa gulu loti lifufuze chenicheni pa imfa ya Mutharika koma a banja la malemuyo, motsogozedwa ndi mchimwene wake, Peter, adati kafukufukuyo n’kungotaya nthawi.

 Mtsogoleri wa mgwirizano wa mabungwe omwe siaboma la Council for Non-Governmental Organisations (Congoma), Voice Mhone, wati amabungwe achitapo kanthu ngati a banja la Mutharika akane kafukufukuyo.

“Ife tikudabwa kuti kodi a banja akukaniranji. Kufufuzako n’koyenera ndipo tikuwapempha alole zomwe boma likufuna.

“Amalawi sakudziwabe mmene Mutharika adamwalirira,” adatero Mhone.

 Mkulu wa bungwe loona ufulu wa chibadwidwe la Malawi Watch, Billy Banda, wati Mutharika adasankhidwa ndi anthu kotero anthuwo adziwe za imfa yake.

“Ndikukhulupirira abanjawo chilipo akubisa. [Boma likafufuza] timva zambiri monga tsiku lenileni lomwe adafera, komwe adamwalirira komanso momwe zidachitikira kuti amwalire.

“Timvanso za chuma chake ndiye a banja asakane,” adatero Banda.

Akumudzi sadziwa

Mfumu Yaikulu Malemia ya m’boma la Nsanje yati anthu akumudzi sadziwabe tsiku lomwe Mutharika adamwalirira komanso matenda omwe adapha mtsogoleriyo kotero boma lisagonjere.

Iye wati zimamveka kuti kuti kunyumba ya boma komwe Mutharika adagwera kunalibe galimoto za boma zothandiza pa zadzidzidzi monga matendawa.

Malemia watinso nyumba zoulutsira mawu zakunja zidalengeza kuti Bingu wamwalira pomwe kuno akuluakulu amakana, kotero zenizeni sizinadziwikebe.

“Ngati a banja akudziwa abwere poyera, apo ayi kafukufuku achitike,” adatero Malemia.

Charles Kabaghe wa m’mudzi mwa Mkombanyama kwa T/A Mwaulambia m’boma la Chitipa wati ngakhale kafukufukuyo akhale wolira ndalama, achitike.

“Zikumveka kuti Bingu adamwalirira kunyumba ndipo adangopita ndi thupi ku South Africa pomwe aboma panthawiyo adakana; izi zikutisokoneza.

“Nalo tsiku lomwalira silikudziwika. Boma lifufuze tidziwe mutu weniweni,” adatero Kabaghe.

Aubrey Jeke wa m’mudzi mwa Sambani kwa T/A Mlolo m’boma la Nsanje wati kumeneko anthu akufuna kudziwa zambiri.

Iye wati kumeneko zokamba n’zambiri ndipo mpofumika boma likumbe nkhaniyi mwatsatanetsatane.

Boma limvere a banja

Koma T/A Mwakaboko wa m’boma la Karonga wati boma limvere zomwe abanja akunena chifukwa ngati iwo sakufuna kuti kafukufukuyo achitike sibwino kukakamira.

“Mutharika adaikidwa kumalo ake ku Thyolo, malo amenewo si aboma ndiye a banja ali ndi ulamuliro onena zomwe afuna,” adatero Mwakaboko.

Pulezidenti Banda adasankha gulu la anthu asanu ndi atatu kuti lifufuze za imfa ya Mutharika.

Gululi likutsogoleredwa ndi woweruza milandu ku bwalo lalikulu Elton Singini.

Enawo ndi Dr. Charles Dzamalala, yemwe adali mkulu wa apolisi, Joseph Airon, Dr. Tionge Loga, Dr. Elizabeth Sibale, Fr. Joseph Mpinganjira, Brian Nyasulu, Esther Chioko ndi woimira anthu pamilandu, Jabber Alide.

Lachisanu pa 15 akuchokera ku Mangalande, Banda adauza atolankhani kuti kafukufuku akhalapo pa imfa ya Mutharika.

Mayi Banda adati Mutharika adali mtumiki wa dziko lino kotero anthu akuyenera kudziwa chomwe chidamukokera ku masano.

Izi zidaipira mchimwene wa malemuyo, Peter, yemwe adauza nyumba youlutsira mawu ya Voice of America kuti sakumvetsabe zomwe boma likufuna pa nkhaniyi.

Iye anati ngati boma likufuna kudziwa chilungamo likafunse dotolo yemwe adalipo pomwe Mutharika amatengeredwa kuchipatala.

Iye adati ngati a banja ali okhutira ndi lipoti la imfa ya Mutharika palibenso chifukwa choti boma litaye nthawi kufufuzabe.

“N’zamkutu komanso zopanda ntchito. Pali atsogoleri ambiri omwe amwalira m’maiko osiyanasiyana, kodi ndi kangati padali kafukufuku wa boma? Kafukufukuyu ndi wa zii. Ine monga wamkulu kubanja ndikukhulupirira kuti ndizopanda ntchito komanso kungotaya nthawi.

“Ngati banja lakhutira bwanji boma likufunitsitsabe kupeza chomwe chidapha mtsogoleriyo? Akufuna chiyani?” adadabwa Mutharika.

Related Articles

Back to top button