A Chakwera ati sasaina bilu la antchito

Mabungwe oyimira anthu ogwira ntchito ati ndiokondwa kuti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera amva kulira kwawo, kuti asasaine lamulo, lomwe, mwa zina, likukamba za sitalaka ya ogwira ntchito, lomwe Nyumba Yamalamulo idavomereza sabata ziwiri zapitazo.

Lamulolo likuti olemba ntchito adzidula malipiro a ogwira ntchito akakhala pa sitalaka kopitilira masiku atatu.

Kuchita sitalaka ndi ufulu wa Amalawi

Koma Lachitatu, pomwe bungwe loimilira mabungwe omenyera maufulu aanthu a pantchito la Malawi Congress of Trade Unions (MCTU) limakonzekera zionetsero zotsutsa lamulolo, a Chakwera adaitanitsa nthumwi za bungwelo ndi kulilonjeza kuti sasayina lamulolo ndipo m’malo mwake alibwezera ku Nyumba ya Malamulo.

Mlembi wabungwelo a Madalitso Njolomole komanso mneneri wa a Chakwera a Brian Banda adatsimikiza kuti a Chakwera alonjeza kusasaina lamulolo mpaka atakhutira kuti ndondomeko yoyenera idatsatidwa.

“Ndife okondwa kuti a Pulezidenti amvera pempho lathu. A Chakwera adalonjeza kuti sangasayine lamulo lomwe silidapangidwe mwa ndondomeko,” adatero a Njolomole.

Koma wachiwiri kwa nduna ya zantchito a Vera Kamtukule adauza Nyumba ya Malamulo kuti mbali zonse zokhudzidwa zidafusidwa maganizo pa lamulolo.

Mkulu wa bungwe la olemba anthu ntchito la Employers Consultative Association of Malawi (Ecam) a George Khaki adavomereza kuti unduna wa zantchito udawaitana pamodzi ndi a MCTU ku zokambirana koma sadamvane chimodzi.

Pomwe a Kamtukule adati sizitengera kuti mbali zokambirana zamvana kapena ayi kuti boma lipitilire ndi kupititsa lamulo lo ku Nyumba ya Malamulo komanso bungwe lalikulu loona zantchito padziko lonse lapansi limavomereza kuti munthu asalandile malipilo m’masiku omwe sadagwire ntchito.

Pa 8 July 2021, pomwe Nyumba ya Malamulo idavomereza lamulolo, aphungu otsutsa boma a Democratic Progressive Party (DPP) ndi United Democratic Front (UDF) adatuluka m’Nyumbayo potsutsana ndi lamulolo.

Bungwe la MCTU lidaimililidwa ndi a Joseph Kankhwangwa, a Jessie Ching’oma, a Limbani Kachali, a Dorothy Ngoma ndi a Overton Simbeye pomwe Ecam idayimililidwa ndi a Emmanuel Banda komanso a Beyani Munthali.

Bungwe loimira aphunzitsi la Teachers Union of Malawi (TUM) nalonso ndilokwiya ndi lamulolo chifukwa ati lakonzedwa dala pofuna kuopseza aphunzitsi kuti asapitirize kudzimenyera ufulu woti azilandira mswahara wa ukadziotche kapena ndalama zogulira zodzitetezera ku matenda a korona.

Koma mkulu wa bungwelo a Willie Malimba adagwirizana ndi maganizo a a Njolomole pa kusasaina lamulolo.

“N’chifukwa chiyani lamulolo likubwera pomwe aphunzitsi adakali ndi nkhawa za mswahara wa ukadziwotche ndi ndalama zogulira zodzitetezera ku mlili wa korona? Akufuna kuti atseke pakamwa aphunzitsi,” adatero a Malimba.

Mkulu wa bungwe la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) a Michael Kaiyatsa adati lamulolo litayamba kugwira ntchito, ufulu wa ogwira ntchito ukhoza kutha.

“Lamulolo ndi lachibwana kwambiri chifukwa likutseka pakamwa ogwira ntchito ngati aphunzitsi. Apapa sangalankhulenso kalikonse ngakhale ataona kuti akuponderezedwa zomwe ndi  kuphwanya ufulu wa anthu,” adatero a Kaiyatsa.

Kadaulo pa kayendetsedwe ka zinthu m’dziko a Boniface Chibwana yemwenso amagwira ntchito ku bungwe loona za mtendere ndi chilungamo la CCJP adati Amalawi akalekelera kuti lamulolo liyambe kugwira ntchito, apantchito onse ali pamoto.

“Ndi ufulu wa anthu kuchita chionetsero kapenanso kunyanyala ntchito kumene ngati sakugwirizana ndi machitidwe a owalemba ntchito ndiye kutero ndi kupanganso lamulo lolanda ufulu wa antchito,” adatero a Chibwana.

Related Articles

Back to top button