Nkhani

A Escom adziwe kuti takwiya—Kapito

Si zachilendonso, nyimbo yomwe aliyense akuimba ndi kuzimazima kwa magetsi. Mmalo mopereka magetsi tsiku lililonse monga anenera, ayamba kupereka mdima tsiku lonse.

Izi sizikukhumudwitsa anthu okha, nawo amabungwe akwiya nazo.

Kapito: Osasekerera zimenezi
Kapito: Osasekerera zimenezi

Monga akunenera mkulu wa bungwe loona ufulu wa anthu ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito, Escom isimba tsoka posakhalitsa.

“Escom imva nkhwangwa ili m’mutu. Zafika pokwana ndipo tatopa ndi kulira. Uwu ndi mtopola ndipo zithera pa wina,” watero Kapito.

Kapito wati vuto ndi Amalawi chifukwa safuna kugwirizana zinthu zikafika povuta monga zilili pano.

“Tigwirane manja, tiyeni tionetse mkwiyo wathu ndipo awa a Escom adziwenso kuti takwiya. Si bwino kusekerera zotere, talankhula ndipo tatopa. Panopa tiyeni tichitepo kanthu,” adatero Kapito.

Naye mkulu woona mabungwe a mabizinesi ang’onoang’ono lotchedwa Small and Medium Enterprises Association (SMEA), James Chiutsi, akuti chuma cha dziko lino chikutsika chifukwa makampani ambiri sakugwira ntchito.

Chiutsi wati Escom ikuyenera kupeza njira zina zothandizira anthu kusiyana n’kumawanamiza nthawi zonse.

“Anzathu amapanga magetsi kuchokera kudzuwa komanso kumphepo. Ife tikudalira magetsi opukusidwa ndi mphamvu ya madzi, kodi nanga madziwo akadzaphwera ndiye kuti tidzakhalanso ndi magetsi?” adadabwa Chiutsi.

“Panopa zinthu zaipa, makampani alowa pansi ndi pafupifupi theka. Ena atseka makampani awo chifukwa sangakwanitse kugwiritsira ntchito injini za magetsi (generator). A mabutchala nyama ikuonongeka, ometa ena asiya. Kodi dziko lingatukuke bwanji? Komanso muyembekezere kuti munthu yemweyo akuyenera kupereka ndalama ya lendi. Kodi aipeza kuti,” adatero Chiutsi.

Mkuluyu ndi Kapito apempha boma kuti lichitepo kanthu pa nkhaniyi kuti Amalawi aone kusintha pa nkhani ya kuthimathima kwa magetsi.

Related Articles

Back to top button