Nkhani

A Malawi adalimba nazo chaka chatha

Ululu, kulavulagaga ndi kupala moto kudalipo mchaka chomwe changothachi monga momwe akadaulo mnthambi zosiyanasiyana akunenera kuti padalibe popumira koma kubanika kokhakokha.

Malinga ndi akadaulo a zamaufulu, zaumoyo ndi oyimira anthu ogula ndi kugwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana, Amalawi adawawulidwa, makamaka pa mmene ogulitsa zinthu amakwezera mitengo ndi mmene ntchito zina monga zaumoyo, ufulu wa anthu, magetsi ndi madzi zidayendera m’chaka changothachi.

Madzi ndi moyo: Mnyamatayu sakadachitira mwina koma kupeza njira yomwera madzi ku Nkhotakota
Madzi ndi moyo: Mnyamatayu sakadachitira mwina koma kupeza njira yomwera madzi ku Nkhotakota

Za umoyo

Chaka cha 2015 ndi chaka choyamba chomwe tidaona anthu odwala m’chipatala akudya kamodzi patsiku osatengera mtundu ndi kuchuluka kwa makhwala omwe akulandira pavuto lawo.

Chaka chomwechi ndicho kudali chionetsero cha anamwino ndi azamba pa nkhani yoti boma silikuwalemba ntchito ngakhale kuti adachita ndi kumaliza maphunziro awo a ntchitoyi panyengo yomwenso ogwira ntchito zachipatala ali operewera.

Malingana ndi mkulu wa anamwino ndi azamba, Dorothy Ngoma, cholinga cha chionetserochi chidali kupempha boma kuti lilembe ntchito achipatala omwe adamaliza maphunziro komanso libweze ganizo loti anthu odwala azidya kamodzi patsiku.

Iye adatinso nkhani ina yodandaulitsa idali kusowa kwa mankhwala m’zipatala, zomwe zidachititsa kuti anthu osauka asakhale ndi mwayi wolandira thandizo loyenera akadwala.

“Chomwe ife tikufuna n’chakuti anamwino ndi azamba onse omwe sadalembedwe ntchito alembedwe komanso chilinganizo choti anthu odwala azilandira chakudya kamodzi m’zipatala chibwezedwe chifukwa munthu wodwala amafunika chakudya chokwanira kuti mankhwala agwire bwino ntchito m’thupi,” adatero Ngoma.

Mkulu wa bungwe loyang’anira za ufulu wa anthu pa nkhani za umoyo, Charles Nyirenda, adati kafukufuku yemwe bungweli lidachita m’zipatala zingapo m’dziko muno adaonetsa kuti mankhwala m’zipatalazi mudalibe. zaumoyo Peter Kumpalume adati mankhwala adasowa m’zipatala kaamba ka anthu ena oipa mtima omwe amaba mankhwala n’kumakagulitsa posaganizira miyoyo ya anthu.

Ndunayi idalonjeza akuti ithana ndi anthu onse omwe akukhudzidwa ndi zachinyengo cha mtundu uliwonse muundunawu.

Za maufulu

Nkhani ina yomwe idakhoma misomali yowawa pamitu pa Amalawi ndi ya maufulu omwe akatswiri akuti sadalemekezedwe monga momwe zimayenera kukhalira.

Malingana ndi mmodzi mwa akuluakulu oyang’anira za maufulu, Billy Mayaya, maufulu ambiri adaphwanyidwa, monga ufulu wa maalubino omwe akuti amaphedwa ndi kuchitidwa nkhanza za dzaoneni.

Iye adatinso ufulu wina ndi wolandira nthandizo la mankhwala akadwala komanso chakudya.

Mayaya adatinso m’chakachi, boma lidaonetsa kusalabadira maganizo ndi zofuna za anthu makamaka pa mmene lidagulitsira banki ya boma ya Malawi Savings anthu ndi magulu osiyanasiyana atayesetsa kuletsa.

Mkuluyu adatinso ufulu wa atolankhani udaponderedzedwa kwambiri m’chakachi ngakhale kuti boma lidalonjeza kuti lidzapititsa patsogolo ufulu wa atolankhani kuti azidzatha kufufuza ndi kuulutsa nkhani popanda kusokonezedwa.

“Mwachitsanzo, wayilesi ya Zodiak idaletsedwa kulowa kunyumba ya boma kuli zochitika pomwe wailesi ndi nyuzipepala zina zidaloledwa, kumeneku n’kuwaphwanyira ufulu wotola ndi kuulutsa nkhani,” adatero Mayaya.

Nduna yofalitsa nkhani za boma, Jappie Mhango, adati mpofunika kumpatsa nthawi yoti alingalire zonsezi asadayankhepo kalikonse kuti poyankha atsekeretu maenje onse.

 

Magetsi ndi madzi

Mawu oti madzi ndi moyo adasanduka nthano m’chaka chimenechi polingalira mavuto omwe adalipo kuti mpaka anthu kufika pomamwa madzi a m’zitsime ndi zithaphwi chifukwa mipopi imakhala youma nthawi zambiri.

Malinga ndi akuluakulu a makampani opopa ndi kugawa madzi osiyanasiyana, vutoli lidakula kaamba ka vuto la magetsi omwenso adamvetsa kuwawa Amalawi.

“Madzi timachita kupopa ndi mphamvu ya magetsi ndiye ngati magetsi kulibe, simungayembekezere kuti tipopa madzi okwanira n’chifukwa mumaona kuti madzi pena atuluka pena asiya,” adatero mmodzi mwa akuluakulu a makampaniwa, Alfonso Chikuni, wa Lilongwe Water Board.

Mkulu wa bungwe loyang’anira za anthu ogula ndi kugwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana, John Kapito, adati kulanda anthu madzi ndi magetsi ndi chilango chowawa kwambiri potengera ndalama zomwe anthuwa amapereka kumakampaniwa.

“Chodabwitsa n’chakuti mabilu a madzi ndi magetsi mmene alili kukwera chonsecho nthawi zambiri kumakhala kulibe. Anthu amangokhalira mumdima ndi kumwa madzi osalongosoka,” adatero Kapito.

Anthu ambiri makamaka a mabizinesi adandandaula kuti kuthimathima kwa magetsiwa kudasokoneza bizinesi moti ena adataya katundu wambirimbiri yemwe adaonongeka panyengo yomwe kudalibe magetsi.

Za makhalidwe

Kapito adati moyo m’chakachi udawawa zedi potengera momwe mitengo ya zinthu imakwerera pomwe mapezedwe a ndalama adali ovuta kwambiri.

Iye adati kusakolola bwino kwa chaka chatha, kuvuta kwa malonda a fodya ndi mabala a ‘Cashgate’ ndi zina mwa zomwe zidachititsa kuti m’matumba mwa anthu muume, koma izi sizidamange buleki ya kakwenzedwe ka mitengo ya katundu.

“Kunena zoona Amalawi adamva ululu m’chaka chimenechi. Ndalama zimasowa koma si momwe zinthu zimakwerera mtengo. Kayendetsedwe ka chuma nako kadali kodwalitsa mutu; zimangokhala ngati palibe woyendetsa,” adatero Kapito.

Iye adati chodandaulitsa kwambiri n’chakuti mayankho omwe ankaperekedwa pamavuto onsewa sadali ogwira mtima, mmalo mwake zimakhala ngati kunyogodola anthu omva kale kuwawa.

Chiyembekezo mu 2016

Akuluakuluwa adati Amalawi akufunika zakupsa m’chaka chomwe tayambachi cha 2016 monga kusintha momwe zinthu zimayendetsedwera chaka chatha komanso kupatula ndale ndi kayendetsedwe ka boma.

Kapito adati ali ndi chiyembekezo kuti chaka chino, boma lichita chotheka kuchita kafukufuku wokwanira ndi kuweruza milandu ya ‘Cashgate’ kuti maiko omwe adanyanyala kuthandiza dziko lino abwererenso.

Mayaya naye adati boma likhwimitse ndondomeko zotetezera maufulu a anthu, makamaka maalubino, ana ndi amayi omwe nthawi zambiri amakhala kunsonga ya nkhanza zosiyanasiyana.

Nyirenda adati ali ndi chikhulupiriro kuti zomwe adalonjeza Kumpalume zothana ndi katangale muundunawu zichitika m’chaka chimenechi kuti nkhani za umoyo zipite patsogolo, osati momwe zidalili chaka chathachi. n

Related Articles

Back to top button