Nkhani

A maufulu ayamikira MCP

Listen to this article

Akatswiri andale kudzanso mabungwe oimira ufulu wa anthu mdziko muno ayamikila chipani chachikulu chotsutsa boma cha Malawi Congress Party (MCP) powonetsa chitsanzo chabwino kwambiri potsata ndale za demokalase posankha anthu m’maudindo kupyolera mnjira yovomelezeka ya chisankho.

Chakwera (wachiwiri kuchokera ku manja) limodzi ndi mkazi wake Monica komanso akuluakulu ena kumsonkhanowo
Chakwera (wachiwiri kuchokera ku manja) limodzi ndi mkazi wake Monica komanso akuluakulu ena kumsonkhanowo

M’miyezi iwiri yotsana ya July kudzanso August chaka chino, MCP   yachititsa zisankho mu zigawo za kumwera ndi pakati. Ndipo m’menemo chaika anthu atsopano m’mipando yosiyasiyana oyendetsa chipanichi mzigawozo.

Katswiri wa ndale ku sukulu ya ukachenjede ya University of Malawi chigawo cha Chancellor College a Mustapha Husseni, ati zomwe ikuchita MCP ndiye zoyenera komanso zofunika kwambiri pa ulamuliro wa demokalase mchipani.

“Chipanichi mpofunika kuchiyamikira pazomwe chikuchitazi. Chikuchita ndale zololerana za-’intraparty democracy’, ndipo ife tingoti asaleke zimenezi chifukwa kumeneku ndiye kulimbitsa chipani mnjira yoyenera,” atero a Husseni.

Malinga ndi mneneli wa MCP a Jessie Kabwira,  chipanichi chichititsanso chisankho chonga chomwechi ku chigawo cha kumpoto. Iwo ati akuchita zimenezi kuti chipanichi chikhale cholimba, ndicholinga chakuti pomadzafika nthawi ya chisankho chachikuru chosankha prezidenti wadziko, aphungu, kudzanso makhansala mu 2019, chidzakhale cha mphamvu kwambiri m’madera onse adziko lino.

Mkulu wa Centre for the Deveopment of People (Cedep) , a Gift Trapence,  sadabise mau kukhosi ponena kuti zimenezi sizachilendo ai, kaamba kakuti ndikofunikiradi  kutero, maka poyang’anila kuti eni ake a zipani za ndale ndi anthu wamba omwe ndiwochuruka.MCP_women_dancing

“Zotsatira zake nzakuti zinthu zikamayenda motero, anthu ambiri amakhala nacho chikhulupiliro chipani choterocho. Iwo amadziwa kuti pakutero icho  chikutsatsa njira zabwino za democracy. Ndiponso izi sizifunika mchipani mokhamo ai, komanso ngakhale dziko lonse,” adatero a Trapence.

Nawonso a Timothy Mtambo, a Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), potsilira ndemanga afotokoza kuti MCP yawonetsa kukhwima nzeru mu ndale za demokalase poika anthu m’maudindo mchipanichi kudzera mnjira yovomelezeka yachisankho.

“Zoonadi iyi ndi njira yabwino kwambiri, kusiyana ndikungoloza ndi chala kapena kumangosankhana ndi pakamwa pokha.  Kuwonjezera pamenepa, ife tikupempha kuti zisathere pa maudindo ang’onoang’ono okhawa  ai,  komanso ngakhale wa pulezident ndi ena otere, zidzikhalanso chimodzimodzi. Pamenepa sitikunena MCP yokha ai, komanso zipani zonse za ndale mdziko muno,” atero a Mtambo.

A Mtambo anatinso ndizodabwitsa kuti MCP yomwe inkakanitsitsa kubweretsa ndale za demokalse mu ulamuliro wake wa  chipani chimodzi,  lero lino ikuposa zipani zina, pokhala patsogolo kuwonetsa chitsanzo chabwino pa ndale za zipani zambiri mdziko muno.

A Mtambo anadzudzulanso mchitidwe omwe akuti zikuchita zipani zina mdziko muno, posankha mwana kaya mchimwene wake wa pulezident wa chipanicho kukhala mulowa malo, pomwe mtsogoleriyo akutula pansi udindo.

“Ngakhale kuti mdziko muno muli ufulu wakuti wina aliyense akhoza kupikisana nawo pa udindo wina uliwonse, komabe, mchitidwe okhala ngati waufumu, osiilana udindo muzipani za ndale ukukhumudwitsa anthu, komanso kuwopseza chitetezo cha ndale za democray.”

“Zoterezi sizabwino nkamodzi komwe. Ndipo zitheretu. Apatu  sitikunena muchipani cha ndale chokha ai, komanso ngakhale dziko lonse la Malawi. Tisawumilize anthu kuchita zomwe mwina iwo sakufuna. Alekeni otsatila chipani  asankhe okha munthu yemwe akumufuna kuwatsogolera mchipanimo.  Ndiye tikawonetsetsa, komanso kunena mwa chilungamo poyelekeza ndi zipani zina,  zimenezo sitinaziwone pakali pano mu MCP. Pachifukwachi ndithu tikuwayamikira komanso kuwalimbikitsa kuti zimenezi apitilize,” adatero Mtambo.

Related Articles

Back to top button