Columns

Abambo, alekeni mayiwo atukuke

Listen to this article

Akutitu m’makomomu alipo abambo omaipidwa ndi kutukuka kwa mkazi wawo.

Mkazi akati ayese kupitiriza sukulu, abambo oterewa amaletsa kapena kuchita chilichonse chomwe angathe pomulepheretsa mayiyo kukalowa m’kalasi.

Ena kungovomereza kokha kuti mayi achite bizinezi, ayinso. Ndiye kuti ngati alibe mpamba bambo sangamuthandize ataa! Mayi uja akalimbika payekha mwina kupeza ngongole kumabanki akumidzi achuluka masiku anowa, bambo amangosolola ndalama zija n’kuona nazo chochita.

Ena abambo ntchito yomweyi kuti mkazi angopezeka paofesi ndi mavutonso. Chofuna chawo n’chakuti mayi azingokhala pakhomo.

Mantha a abambo oterewa amati mayi akatalikira ndiye kuti mwina azichita zibwenzi. Ena amati mayi akayamba kudziimira payekha kumbali ya ndalama ndiye kuti azikula mtima.

Atatero mayiyo kungakhale kulakwitsa. Koma kunena zoona abambo amaganizidwe oterewa ngobwezeretsa chitukuko mmbuyo, okhomerera komanso odzikonda.

Mtima wofuna kulamulira moyo wa mayi poyesetsa kuti muchilichonse azidalira bambo ndi mtima wachabe.

Kutereku kumakhala kuonetsetsa kuti mayi uja moyo wake uzizungulira bamboyo. Akafuna mchere, kukonza tsitsi ndi zina zotero azingotsamira bambo.

Ndipo zikatere kumakhala kovuta kuti mayi achoke pabanja ngakhale zinthu zitavuta chotani chifukwa amadziwa kuti akangochoka pakhomo kapena kusemphana maganizo ndi bamboyo ndiye kuti mchere usokonekera.

Chikondi anzanga sichitere. Sumafuna mnzako akhale mmphawi mwadala ndi cholinga choti moyo wake uzilamuliridwa ndi iwe.

Komanso kuganiza kotero n’kobwezeretsa chitukuko mmbuyo chifukwa banja loti likanapindula ndi ndalama zoonjezera zochokera kwa mzimayi, limangodalira ndalama za munthu mmodzi.

Kuonjezera apo, mchitidwewu suganizira za mawa kuti bambo atamwalira mayi ndi ana zidzawathera bwanji?

Ena abambo abizinezi mkazi sadziwa n’komwe kuti zinthu zimayenda bwanji kotero kuti imfa ikatenga bamboyo, bizinezi nayo imathera pompo.

Tonse tingakonde kuti obweretsa ndalama pakhomo ndiye azimwalira komalizira, koma moyo suyenda choncho. Aliyense amanyamuka mwadzidzidzi.

Tsono ukachita zinthu momati banja lonse lizidalira iwe, ukamwalira anzakowo zidzawathera bwanji? Banjalo lidzakhala paumphawi waukulu chifukwa choti mwamuna anali ndi nkhawa zopanda pake.

Related Articles

Back to top button
Translate »