Chichewa

Abambo odzikhweza akuchuluka

Listen to this article

 

Kafukufuku wa apolisi m’dziko muno waonetsa kuti abambo 90 ndiwo amadzipha pa anthu 100 alionse amene amatenga miyoyo yawo podzikhweza kapena kudzipha m’njira zina.

Malinga ndi mneneri kulikulu la polisi, Nicholas Gondwa, abambo ambiri amalimba mtima ndi kudzipha kusiyana ndi amayi.

suicide

“Koma amayi ndi olimba mtima, amakumana ndi nkhanza zambiri, koma ndi ochepa omwe amadzichotsera moyo,” iye adatero pocheza ndi Msangulutso.

Polankhulapo, mneneri wa apolisi m’chigawo cha kumpoto, Maurice Chapola, adati abambo ambiri akakumana ndi nkhaza za m’banja amathamangira kudzipha mmalo mokadandaula kunthambi ya polisi ya Victim Support Unit (VSU).

Chapola adati abambo khumi ndiwo amakadandaula ku VSU mwa anthu 100 alionse.

Kondwani Machano yemwe ndi bambo wa ana awiri, adati abambo amaopa kupita kupolisi akakhala ndi nkhawa kuopa kuukiridwa komanso chifukwa ambiri mwa iwo sadziwa kulankhula.

Ndipo katswiri woona zakaganizidwe (psychiatrist), yemwenso ndi mkulu wa chipatala cha St John of God m’mzinda wa Mzuzu, Charles Masulani Mwale, adati abambo ambiri akakhala ndi mavuto a m’maganizo, sagawira anzawo za nkhawazo kuopa kuoneka opusa.

“Abambo amaopa kuoneka opepera akauza ena za mavuto awo ndipo amawasunga m’maganizo, pomwe amayi amagawana nkhawa zawo,” Masulani adatero.

Iye adati abambowa amakakamira kuthana nawo okha mavuto omwe ali nawo.

Masulani adati kafukufuku waonetsa kuti ngakhale amayi ambiri ndiwo amalingalira zodzipha, ambiri mwa iwo sadzipha kaamba koti amatsatira njira zozizira zodziphera pomwe abambo omwe amalingalira zodzipha amagwiritsa ntchito njira zoopsa pochotsa miyoyo yawo.

“Tinene kuti amayi amangoopseza kuti adzipha kusiyana ndi abambo omwe akalingalira, amachotsadi moyo wawo m’njira zoopsa,” Masulani adatero.

Iye adati vuto lodzipha ndi lalikulu m’maiko otukuka kumene ati kaamba koti anthu sadziwa kopita akakhala ndi mavuto a m’maganizo.

“Sitidazolowere kuti tikakhala ndi nthenthe kapena kupanikizika m’maganizo tiyenera kupita nazo kuchipatala, koma izi zimafunika thandizo lamsanga la akatswiri odziwa za kaganizidwe,” Masulani adatero.

Iye adati pachipatala cha St John of God amayi ambiri ndiwo amafuna thandizo kusiyana ndi abambo.

Masulani adati ambiri mwa amayiwa amavutika m’maganizo chifukwa cha mavuto a m’banja komanso umphawi.

“Ambiri amati mwina angodzipha chifukwa umphawi wafika povuta ndipo chilichonse chomwe ayesa sichikuyenda,” Masulani adatero.

Iye adaonjezera kuti ena mwa amayi omwe ali ndi ana opuwala amakhalanso ndi maganizo odzipha maka amuna awo akamawanyoza kuti amabereka ana otero. n

Related Articles

Back to top button
Translate »