Nkhani

ACB idayamba kale kufufuza Chaponda

Listen to this article

Nthambi yofufuza za ziphuphu ya Anti-corruption Bureau (ACB) yati idayamba kale kufufuza nkhani ya momwe bungwe la Admarc lidagulira chimanga m’dziko la Zambia.

Mkulu wa ACB Lukas Kondowe adanena izi Lachitatu, patangotha masiku angapo kuchokera pomwe komiti imene lidasankhidwa ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti lifufuze ngati nduna ya za malimidwe George Chaponda ikukhudzidwa pankhani yoti bungwe la Admarc lidasokoneza zina pogula chimangacho kupyolera mu kampani ya Kaloswe Courier and Commuter Services ya ku Zambia.

Afufuzidwe: Chaponda

Mwa zina, gululo, limene limatsogoleledwa ndi Anastazia Msosa, lidapempha Mutharika kuti ACB ifufuze momwe nkhaniyi idayendera. Koma Kondowe adati adayamba kale izi.

“Tidayamba kale ngakhale mtsogoleri wa dziko lino asadakhazikitsenso komiti yapadera. Choncho tingopitiriza basi,” adatero Kondowe.

Polankhula ndi mtolankhani wathu, Kondowe adati adangomva pawailesi za kupsa kwa ofesi ya Chaponda Lachiwiri ndipo adati akudikira lipoti la momwe maofesi a Chaponda ndi akuluakulu ena adapsera.

“Sitikudziwa ngati zomwe tikadafuna m’kafukufuku wathu kumeneko, zaonongeka nawo ndi motowo,” adatero Kondowe.

Motowo udaononga ofesi ya nduna

Malinga ndi mkulu wa apolisi Lexten Kachama amene adafika pamalo a ngoziyo adati apolisi akufufuzabe chidayambitsa motowo cha m’ma 11 koloko m’mawa.

Motowo udadzetsa mtsutso  pakati pa Amalawi pamene ena ankati udabuka pofuna kusokoneza umboni pomwe ena ankati ndi ngozi chabe.

Polankhulapo, mmodzi wa a mabungwe omwe si a boma omwe adakatenga chiletso mwezi watha kuti ndunayi ayiimitse kaye pantchito mpaka kafukufukuyu atachitika Moses Mkandawire adati kuyaka kwa ofesiku kukufunika kufufuzidwanso mwapadera.

Mkandawire, yemwe ndi mkulu wa bungwe loona za kakhalidwe ka anthu ya Church and Society mu sinodi ya Livingstonia, adati pakadalipano ndi zovuta kuloza zala munthu kuti ndiye wayatsa motowo.

“Sitingaloze zala munthu kuti ndiye wayatsa moto; koma chofunika ndi kafukufuku   wina kuti ofesiyi idayaka bwanji panthawi ngati ino pomwe ili mkamwamkamwa mwa anthu? Bwanji siyidayake ofesi ya zofalitsa nkhani kapena ofesi ina? Kodi tingati izi zangochitika?” adadabwa Mkandawire.

Iye adati chopweteka kwambiri n’choti failo ndi uthenga wambiri waboma waonongeka ndi motowo zomwe zingasokoneze ntchito za boma zomwe zimayenera kupitilizidwa  ndi anthu osiyanasiyana.

“Izitu nzopweteketsa ana athu chifukwa tawaonongera uthenga wofunika womwe akadadzaugwiritsa ntchito mtsogolo muno kaamba koti zinthu zathu zambiri sizili pa intaneti n gati maiko aanzathu,” adatero Mkandawire.

Komabe Mkandawire adayamikira Mutharika pokhazikitsa komiti yapaderayo komanso adayamikira zotsatira za kafukufukuyo ati popeza adangotsimikizira zomwe mabungwe omwe siaboma akhala akunena kuti Chaponda ngofunika kufufuzidwa bwino.

Malinga ndi lipotili Chaponda akuyenera kufufuzidwa pa momwe adalowerererapo kuti kampani ya Transglobe ikhale nawo m’gulu logulitsa boma chimanga.

“Pali kukaikitsa pa njira yomwe kampani ya Transglobe idapezera chiphaso chotumizira chimanga kuchokera m’dziko la Zambia kubweretsa kuno, choncho Chaponda akuyenera kufufuzidwa mbali yomwe adatengapo,” idatero lipotilo.

Lipotili lidatinso bungwe la ku Zambia la Zambia Cooperative Federation lomwe adali pamgwirizano ndi bungwe Admarc loperekera chimanga chokwana matani 100 000, lidangoperekapo matani 4 000 okha.

Padakalipano komiti yapadera ku Nyumba ya Malamulo, Lachitatu limayembekezera kutulutsa zotsatira zake.

Poyankha mafunso a komitiyo sabata yatha, Chaponda adati nkhaniyo siyimamukhudza kwambiri chifukwa gawo lake lidali kukambirana ndi nduna ya malimidwe ku Zambia kuti boma la Malawi likufuna chimanga. Za ndondomeko yogulira chimangacho, iye adatero, idali m’manja mwa Admarc.

“Dziko lathu lidali pamoto wa njala. Ngati nyumba ikupsa, mukhonza kuthyola zitseko ndi mawindo kuti mupulumutse mwana amene angafere momwemo. Ndondomeko zina sizinatsatidwe chifukwa tidali pampishupishu,” Chaponda adatero.

Related Articles

Back to top button