Nkhani

Achitira zadama mu basi

Listen to this article

Anthu ena okhala mumzinda wa Mzuzu akhala akuchitira za dama m’mabasi omwe adaimikidwa kumsika wa Zigwagwa pafupifupi miyezi inayi yapitayi.

Mabasiwa, salinso m’manja mwa kampani ya Axa chifukwa banki ya FDH idawagulitsa kwa mkulu wina wa bizinesi yemwe adawaimika ku Zigwagwako poyembekezera kuwagulitsa ndi kuwaphwasula ena mwa iwo.

Imodzi mwa basi amachitiramo zadamayo

Komatu anthu ena apezerapo mwayi wochitiramo za chiwerewere maka yomwe idali ndi magalasi osaonekera mkati, tintedi.

Msangulutso udatsinidwa khutu kuti izi zakhala zikuchitika madzulo komanso usiku ndipo kuti anthuwa amalipira kangachepe kuti apeze mwayi wodzithandiza m’basimo.

Komatu si anthu a zadama okhawa omwe amapumira m’mabasiwo, ngakhalenso ena osowa kogona, adatenga mabasiwo ngati nyumba zogona alendo.

Pomwe Msangulutso udakazungulira pamalopo udapeza mlonda Chimwemwe Kachali yemwe adavomereza kuti wakhala akupezerera anthu akuchita chiwerewere mu imodzi mwa mabasiwo makamaka usiku.

“Anthu amatengerapo mwayi chifukwa ndi yosaonekera mkati ndiye zomwe amachitazo sizimaoneka kunja. Chifukwa choti chitseko chake sichitsekeka, anthu ankangolowamo,” adatero Kachali.

Iye adakanitsitsa zoti adalandirapo ndalama kuchokera kwa anthuwa.

“Mwina popeza miyezi yapitayo tidalipo awiri ndi mnzanga, ndiye kuti mwina ndi yemwe amalandira ndalama;  koma ine sindidalandireko kanthu chifukwa ambiri mwa anthu omwe amachitira zadama mmenemo adali anthu woti timawadziwa ndithu,” adatero Kachali.

Iye adaonjezera kuti zikuoneka kuti ngakhale komwe mabasiwo adali asadagulidwe ndi bwana wake mchitidwewu umachitika chifukwa adabwera ali ndi makondomu ogwiritsidwa ntchito mwa zina.

Apa adatinso masiku ena amapezanso makondomu ogwiritsidwa kale ntchito omwe anthuwo amawataya akamaliza zadamazo.

“Idafika nthawi yoti anthu amakuwa akamadutsa pano kuti m’mabasimu mutuluka mwana ndipo ena amati aphwasulidwe kapena kugulitsidwa mwachangu,” adalongosola Kachali.

Iye adati zitafikapo abwana ake adayesa kuitseka ndi mawaya kuti anthu asamalowe koma sizidathandize chifukwa anthuwo adadula mawayawo.

“Nthawi zina ndikati ndikayendere basi pakati pausiku ndimapeza mwagona anyamata achilendo. Zikatero ndimawathamangitsa. Ambiri mwa iwo amakhala oti athamangitsidwa m’nkhalango ndipo alibe kolowera,” adatero Kachali.

Pocheza ndi tsamba lino, mwini ma basiwo George Biyeni adati adagula mabasi asanu omwe adali a kampani ya Axa kuchokera kubanki ya FDH ndipo adalemba alonda ake awiri oyang’anira mabasiwo koma mmodzi adasiya ntchito.

Biyeni adati mphekesera yoti m’mabasiwo makamaka ya tintediyo mumachitika za dama idamupeza ndipo adangoganiza zoyitseka ndi mawaya kuti anthuwo asamalowemo.

“Ndimati ndikalowa m’basimo, mumaoneka kuti anthu amachitamo zawo ndithu, koma ndikafunsa sindimayankhidwa bwinobwino,” adatero Biyeni.

Iye adati basi yomwe izi zimachitika kwambiriyo waiphwasula tsopano ndipo yomwe yatsala pamalopo ndi yoti omwe adawagulitsawo aikhonza kukonzekera kupita nayo ku Blantyre.

Biyeni adaonjezera kuti n’zovuta anthu a zadamawa kugwiritsa ntchito basi inayo chifukwa mwini wake adaikamo anthu ake angapo omwe akugona momwemo poilondera kwinaku akuikhonza.

Ndipo polankhulapo mneneri wa polisi mchigawo cha ku mpoto Peter Kalaya adati ofesi yake sidalandirepo dandaulo pa nkhaniyi.

“Tikadauzidwa tikadafufuza ndipo ochita zadamawo akadaimbidwa mlandu wa idle and disorderly—kuchita zadama malo osayenera,” Kalaya adatero. 

Related Articles

Back to top button