Nkhani

Adakumana bwanji m’chakacho?

Listen to this article

Ankadzapepesa maliro a mkazi wanga’

Ukwati ndi chinthu chabwino, ndipo Mulungu amasangalala nacho. Chaka cha 2015 Mulungu adadalitsa ena ndi mabanja ndipo lero tingochita molawitsa mwa ochepa amene adalandira madalitso olowa m’banja.

Precious ndi ‘Kachingoni’ kake  patsiku la chinkhoswe
Precious ndi ‘Kachingoni’ kake
patsiku la chinkhoswe

Tiyambe ndi Excello Zidana amene adakumana ndi nthiti yake Katerina Mtambo kudzeranso m’mphamvu ya Mulungu.

Zidana, mkonzi wa pologalamu ya Ulimi Walero ku MBC, adakumana ndi nthiti yakeyi malo angapo koma nthawi yeniyeni idali pamene Katerina amakapepesa Excello pa imfa ya mkazi wake.

Katerina adataya wokondedwa wake chimodzimodzinso Excello. Awiriwa akuti adapepesana za imfayo koma kumapeto kwake adatolana ndi kumangitsa woyera.

‘Kudali kosoketsa nsapato’

Wina waluso pakapezedwe ka namwali ndi Richard Chipuwa, goloboyi wa Be Forward Wanderers.

Kuonongeka kwa nsapato ya Chipuwa udali mwayi, poti pokakonzetsa nsapatoyo adakabatha namwali yemwe adapangitsa naye chinkhoswe m’chaka changothachi.

Kukumanako akuti kudali kosavuta koma kuti asoke Chichewa chokhetsa dovu la Dinnah Hxaviel ndiye idali ntchito yoposa kukhala pagolo.

Ngakhale mayi a njoleyi amaletsetsa mwana wawo kuti asayerekeze kuyenda ndi anyamata, koma nthawi idakwana kutinso makolowo sakadakwanitsa kuletsa pamene adakumana ndi mwamuna weniweniyu.

‘Adali kasitomala wanga wa tchipisi’

Wina ndi Steve Nthala yemwe ndi mkulu wa nyimbo m’gulu la Area 36 Anglican Choir ku Lilongwe amene adapeza njole yomwe idali kasitomala wake wa tchipisi.

Iye akuti adagwa m’chikondi ndi Chrissy Malipa yemwe adali kabwerebwere wa tchipisi chomwe mnyamatayu ankakazinga pachiwaya.

Steve akuti namwaliyu amati akamadzagula tchipisi pachiwaya chake mtima umagunda ndipo amangomuyezera chambiri. Chidali chiyambi mgwirizano wolowa m’banja.

‘Timakayang’ana osewera mpira ku Kasungu’

Ulendo wa timu ya Surestream wokayang’ana osewera m’boma la Kasungu udali waphindu kwa Team Manager wa timuyi Honest Nkhwazi.

Honest adapeza chamwayi kuti asodzekonso Chisomo Nkhoma, yemwe ndi wapolisi papolisi ya Kasungu kuti akhale wachikondi wake. Sadaope yunifomu ya polisi, pali chikondi palibe mantha.

Awiriwa adachititsa chinkhoswe m’boma la Kasungu ndipo amangoyembekezera kuti ukwati tsopano uchitike, abusa agwire ntchito yodalitsa awiriwa.

Awa ndi ochepa chabe amene tidawatulutsa patsamba lino kutifotokozera omwe adakumanirana ndi okondeka awo. M’chakachi achite mphumi ndani? Dzina la ‘Yesu’ ndilo lidachititsa

Akulu adati dzina limapereka kapena kulanda mwayi wa munthu ndipo izi nzoonadi, taonera pa Noel Nthala, yemwe mumzinda wa Lilongwe amadziwika ndi dzina lakuti ‘Yesu’ ndipo ndi mmodzi mwa masapota

akuluakulu a timu ya Silver Strikers.

Anthu ambiri mumzinda wa Lilongwe amakhala ndi chidwi akamva za ‘Yesu’ poganiza kuti mwina ndiye wa ku Yerusalemu ndipo ichi ndicho chidatchukitsa mnyamatayu yemwe pano wapeza nthiti Zuziwe Nyondo.

Kukumana kwa Nthala ndi Zuziwe mwina sikungadabwitse chifukwa monga anthu ambiri mumzindawu amazizwa ndi dzinali n’kutheka namwaliyu naye amafunitsitsa atamuona.

“Ndimamuona ndikamachokera kuntchito koma tsiku lina nditalimba mtima ndidamuimitsa nkumulonjera. Nditamuuza dzina langa adaoneka wodzidzimuka koma ine sindidatengere zimenezo, mtima wanga udali pa iyeyo basi,” adatero Nthala.

Naye Zuziwe adati dzina lokhalo amangolimva koma samadziwa kuti munthu wake n’kukhala mmene amawonekera Nthala, ayi.

“Nanetu ndimamuona akamapita pena kuchoka kuntchito chifukwa komwe ofesi yawo ili n’kufupi ndi nyumba ya achimwene anga ku Area 47 koma ndidalibe maganizo oti munthu wotchukayo ndi iyeyo,” adatero Nyondo. n

Related Articles

Back to top button
Translate »