Chichewa

Adatengera Lucky Dube: Liwonde Chibwe

Listen to this article

Oimba akubadwirabadwira m’dziko muno. Mmodzi mwa oimba omwe adza ndi mkokomo ndi MacDonald Liwonde Chibwe wa ku Mponela m’boma la Dowa koma watambalala mumzinda wa Blantye. DYSON MTHAWANJI adacheza ndi katswiriyu motere:

Wawa, tidziwane…

Chibwe: Mulungu ndi wachikondi
Chibwe: Mulungu ndi wachikondi

Ndine MacDonald Liwonde Chibwe, ndimachokera m’mudzi mwa Chimbudzi, mfumu yandodo Mponela m’boma la Dowa. M’banja mwathu tidabadwa ana asanu ndi awiri ndipo ine ndi wachisanu.

Ndibenthulire chiyambi cha maimbidwe ako.

Chidwi changa pa maimbidwe chidabadwa pomwe ndidali wamng’ono. Kuyambira ndili wamng’ono ndakhala ndikukonda kumvera nyimbo zakunja komanso zam’dziko mommuno. Lucky Dube wa ku South Africa ndi Lucius Banda wa kuno ku Malawi ndiwo adandipatsa chidwi kuti ndikhale ndi loto lodzakhala woimba. M’chaka cha 2013 ndidajambula chimbale changa cha nyimbo choyamba chotchedwa Lingakome. Nyimbo zambiri m’chimbalechi zikuseweredwabe pawayilesi zambiri ndipo anthu akuzikonda. Zina mwa nyimbo zili m’chimbalechi ndi Facebook, Kadende, Hello komanso Mama Africa kungotchulapo zochepa. Zambiri mwa nyimbozi zili m’chamba cha reggae. Kapekedwe kanga ka nyimbo kamagwirizana ndi chamba chimenechi.

Oimba ena oyamba kumene sachedwa kufooka ndipo amazilala msanga. Iwe suchita chimodzimodzi?

Kuimba kuli m’magazi anga kotero ine ndabwera kudzakhazikika pa maimbidwe. Anthu ambiri andilandira pa nkhani ya maimbidwe. Izi zikundipatsa mangolomera kuti ndikhazikika palusoli ndipo sindikubwerera mmbuyo. Pakalipano ndikujambula chimbale chachiwiri chomwe dzina lake ndi Tingathe. Chimbalechi chanyamula uthenga womwe ukugwedeza Amalawi kuti adzuke ndi kuyamba kukonda dziko lawo komanso kugwira ntchito molimbika kuti tithetse mavuto a zachuma omwe tikukumana nawo. Pakalipano ndajambula nyimbo zinayi zomwe zipezeke m’chimbale chimenechi. Nyimbozi ndi Namondwe, Dona, Ndimtima komanso True Love. Nyimbo zinayizi zikuseweredwa kale pawayilesi, komanso zikuchita bwino mupologalamu ya MBC Top 20 pa MBC Radio 2.

Chifukwa chiyani nyimbo zako zambiri zanyamula uthenga wachikondi?

Mulungu ndi wachikondi ndipo sitingalekanitse Iye ndi chikondi. Ngati pali chikondi pakati pa anthu awiri pamalopo pamakhala mtendere. Kotero ndidachiona chofunika kulalikira chikondi kudzera m’nyimbo zanga.

Maloto ako ndi otani?

Masomphenya anga ndi oyambitsa gulu loimba lomwe cholinga chake ndi kuthandiza oimba omwe angophuka kumene. Komanso ndikulingalira studio yojambulitsira nyimbo. n

Related Articles

Back to top button
Translate »