Chichewa

‘Adatuma nthenga kudzandifunsira’

Kudali ku Dedza, mwezi wa October m’chaka cha 2017 pomwe Lucy Mvula adalandira uthenga kuchokera kwa mzake wa Geoffrey Kishombe.

Uthengowo umati Kishombe akulephera kugona kotero akumufuna chibwenzi.

Koma Lucy sadaugwiritse ntchito uthengawo chifukwa choti wobweretsa nthengayo adali ankakonda kuledzera  ndipo pomwe ankapereka uthengawo patsikulo n’kuti atalawa pang’ono.

“Koma nthengayo adabweranso tsiku lina maso ali gwaa kudzatsindika za khumbo la Kishombe. Ndipo adandipatsa nambala ya phone ya nzawoyo ndipo ine ndidapereka yanga,” adatero Lucy.

Lero ndi thupi limodzi: Banja la a Kishombe

Apatu awiriwo adakhala masiku ndithu osayankhulana mpaka pomwe tsiku lina Kishombe adamuimbira Lucy ndipo ichi chidasanduka chizolowezi kufikira tsiku lomwe adagwirizana zoti akumane.

Tsiku lokumana litafika, Kishombe, pamodzi ndi anzake ena awiri adapita kunyumba kwa Lucy kukacheza, zomwe zidachititsa kuti macheza awo agwire moto.

Mosakhalitsa, Kishombe adafunsira ndipo naye Lucy sadazengereze koma kulola.

“Ndidatengeka kwambiri chifukwa cha momwe ankandizondera. Ankakonda kuimba foni kungofuna kudziwa za moyo wanga,” adatero Lucy.

Awiriwo adakhala pa ubwenzi kwa zaka ziwiri kufikira pa November 19 2019 pomwe adalowa m’banja ndipo madyerero adachitikira pa Greek Orthodox Garden, mu mzinda wa Blantyre.

Awiriwo ati mavuto awo amathana nawo poyang’ana kwa Mulungu. Lucy amagwira ntchito yaunamwino ndi uzamba pomwe Kishombe amagwira ntchito ku bungwe la Malawi Bureau of Standards (MBS).

Pakadali pano awiriwo akukhalira ku Chigumula mu m’zinda womwewu wa Blantyre koma Lucy amachokera ku Euthini, mfumu Chindi m’boma la Mzimba ndipo Kishombe amachokera m’mudzi mwa Mwafilaso, mfumu  Kyungu m’boma la Karonga.

Related Articles

Back to top button