Nkhani

Adindo akhudzidwa pa imfa ya Masambuka

Listen to this article

 

Kusowa kwa mnyamata wa chialubino m’boma la Machinga kwavumbulutsa zinthu zoziritsa thupi.

Macdonald Masambuka wa zaka 22 yemwe ankachokera m’mudzi mwa Nakawa, Mfumu Nkoola, m’boma la Machingali adasowa pa 9 mwezi watha.

Adaphedwa: Masambuka

Pofika lero apolisiwa amanga anthu 12 powaganizira kuti akukhudzana ndi nkhaniyi ndipo ena mwa iwo ndi wapolisi, wogwira ntchito zachipatala komanso wansembe.

Zinthu zidayamba kufumphuka pa April 1, pomwe apolisi adatsekera  m’chitokosi wapolisi mnzawo Sajenti Chileka yemwe ankagwira papolisi ya Nselema m’bomalo.

Chileka adatsekeredwa pomwe m’nyumba mwake mudapezeka mafupa a munthu. Wapolisiyo adalondolera anzakewo ku Chikwewo komwe adakwirira thupi  la Masambuka.

Apatu mpomwe zidaululikanso kuti naye wachipatala m’bomalo  pamodzi ndi asing’anga awiri akukhudzidwa ndi nkhaniyi.

Wachipatalayu ndi amene amagwira ntchito yopanga anthu opaleshoni pa chipatala cha Machinga ndipo akuganiziridwa kuti ndiye adasenda ndi kuchotsa mafupa Masambuka.

Anthuwatu akuti adabzala mbatata pamalo pomwe adakwirira thupi la Masambuka atalichotsa miyendo ndi manja.

Koma anthu adadzidzimuka Lolemba lapitali pomwe apolisi adatsekera m’chitokosi wansembe wa Chikatolika Thomas Muhosha pomuganizira kuti adatenga nawo mbali pa imfa ya Masambuka.

Muhosha amagwira ntchito yolalika pampingo wa Mulombozi m’boma la Zomba.

Iyeyu akufufuzidwa ndi apolisi ochokera chigawo cha ku m’mawa atatchulidwa ngati mmodzi mwa anthu omwe adatenga nawo gawo pa nkhaniyi.

Ndipo nawo a mpingo wa katolika sadangokhala chete koma kutulutsa kalata yomwe idasainidwa ndi Bishopu George Tambala wa kudayosezi ya Zomba yemwe adati za Muhosha zisawakhudze.

“Ife ntchito yathu ndiyoteteza miyoyo ya anthu. Pachifukwa ichi ndife odzidzimuka ndi okhumudwa ndi zomwe zachitikazi,” idatero kalatayo.

Padakali pano Muhosha waimitsidwa kaye ntchito podikira kafukufuku wa nkhaniyi.

Polankhulapo  mkulu wa bungwe la anthu a Chialubino la Association of People with Albinism Overstone Kondowe adati ndi zokhumudwitsa kuti okhudzika ndi nkhaniyi ndi abale ake a Masambuka komanso adindo monga apolisi ndi achipatala.

Kuchokera 2014 mpaka lero alubino 21 aphedwa m’dziko muno.

Related Articles

Back to top button
Translate »