Nkhani

‘Admarc isagulitse chimanga kunja’

Listen to this article

Bungwe la Admarc lisatengeke ndi zakuti dziko lino likhoza kukolola chimanga chochuluka chaka chino n’kugulitsa chimanga kunja padakalipano, mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi la CisaNet Tamani Nkhono-Mvula watero.

Nkhono-Mvula adauza Tamvani pomwe Admarc ikulingalira zogulitsa chimanga chimene lidagula ku Zambia kumaiko a Kenya ndi Tanzania. Izi zadza pomwenso mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika atalamula asilikali kuti akhamukire kumalire a dziko lino ndi kugwira ofuna kugulitsa kunja chimanga mozemba. Lamulolo lidadza apolisi atagwira galimoto 17 zimene zimafuna kutulutsa chimanga mozemba.

Zina mwa galimoto zimene zidagwidwa

Iye wati mmera omwe uli mminda usapereke chiyembekezo chabodza kuti Admarc igulitse kunja chimanga.

“Njala ikadalipo. Zonse zidzadziwika bwino kafukufuku womaliza wa zokolola akadzatulutsidwa. Posakhalitsapa timasaka chimanga Amalawi atasauka ndi njala, choncho kuchigulitsa panopa kunja ndi chibwana cha mchombo lende,” adatero Nkhono-Mvula.

Iye adati chimanga sichingasowe msika ngakhale m’dziko momwe muno, koma phuma silingathandize konse.

“Pamene boma lakhwimitsa chitetezo kuti chimanga chisatuluke, pakuyeneranso kukhala chitetezo momwe chimanga chikugulitsidwira m’dziko momwe muno. Pali vuto lalikulu pamene chimanga chochokera kumwera chikukagwidwa ku Karonga,” adatero mkuluyo.

Iye adatinso mpofunika kuti boma kudzera ku unduna wa za malonda kapena malimidwe azipereka ziphaso zapadera kwa anthu ofuna kuchita malonda achimanga.

Ndipo polankhula pomwe amakhazikitsa ntchito ya magetsi m’midzi, Mutharika adati ngakhale maiko a Kenya ndi Tanzania ati akufuna kugula chimanga kuchoka ku Admarc, salola kuti izi zichitike.

“Zidachitikapo mmbuyomu kuti pamene tili ndi chimanga chochuluka tidachigulitsa ku Kenya koma chaka chotsatira kudali njala yadzaoneni mpaka kumakagulanso ku Kenya komweko,” adatero Mutharika, n’kupemphanso Amalawi kuti asagulitse chimanga chawo kwa mavenda koma kudikira misika ya Admarc itsegulidwe.

Wapampando wa nthambi yoyang’anira ntchito za Admarc James Masumbu adati mapulani ogulitsa chimanga ku Tanzania ndi Kenya alipo koma akudikira kuti alimi akolole kaye.

“Panopa, pologalamu yonse yaima chifukwa tikufuna tiyambe takolola kuti tiwone chakudya chomwe alimi akolole kuti tidziwe pomwe chitetezo cha dziko chilili kumbali ya chakudya kenako tidzapanga ganizo lenileni,” adatero Masumbu.

Iye adati kugulitsa chimangachi sikuzungulira mutu koma kuti bungweli lili ndi ngongole yofunika kubweza ndipo ndalama zobwezera ngongoleyi zikhoza kupezeka msanga pogulitsa chimangachi.

Polankhulapo pa ganizoli, wapampando wa komiti yoyang’anira za malimidwe mnyumba ya malamulo Joseph ChintantiMalunga adati ganizo la Admarc lofuna kugulitsa chimangacho ndi labwino polingalira kuti akufunika kubweza ngongole zomwe adatenga zogulira chimangacho.

Wachiwiri kwa mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress Elsenhower Mkaka adati ngati mpata ogulitsa chimangacho ungapezeke, Admarc igulitse koma ndondomeko yake iyende moyera.

“Ndi ganizo lofunikira koma ziyende mwachilungamo komanso zisakwirire nkhani ya kagulidwe ka chimanga ku Zambia yomwe ikadali ikuyenera kuoneka mapeto ake,” adatero Mkaka.

Pali malipoti akuti chaka chino anthu pafupifupi 1 miliyoni akhala ndi njala m’dziko la Tanzania pomwe dziko la Kenya lawona ng’amba yomwe silidawonepo kutanthauza kuti njala ivuta mdzikolo.

Malingana ndi mgwirizano wa maiko a mu Common Market for East and Central Africa (Comesa) maiko amayenera kugwirana manja wina a kapezeka ndi vuto ngati la njala.

Masiku apitawo, apolisi adagwira galimoto zomwe zimafuna kutulutsa chimanga kupititsa ku Tanzania kudzera mmaboma a Karonga ndi Chitipa.

Mneneri wapolisi James Kadadzera adati galimotozo ndi chimanga chomwe akuzisunga kudikira upangili wa boma kuti chimangacho atani nacho ndipo eni galimotozo adzazengedwa mlandu ofuna kuzembetsa chimanga. 

Related Articles

Back to top button