Chichewa

Adzikhweza pamkangano wa madzi osamba ku Nkhatabay

 

Chisoni chakuta banja lina ku Bula, T/A M’bwana, m’boma la Nkhata Bay pomwe mnyamata wa Sitandade 8 wadzimangirira atayambana ndi mlongo wake.

Malinga ndi mfumu Dumbulira ya derali, Chrispin Mwale adayambana ndi mlongo wake pankhani ya madzi osamba.

Mfumuyi idati chifukwa cha ichi mnyamatayo adadzimbuka ndi kupita kutchire.

suicide

“Abambo ake adamutsatira kutchire konko koma adadzawathawanso n’kubwererako. Adafikira kuchipinda chake chogona,” idatero mfumuyo.

Malinga ndi mfumuyo, mayi a mnyamatayo adadabwa pomwe adatuma mwana wina kukatenga chinangwa choti aphike ndipo mwanayo adapeza mbale wakeyo atadzimangirira ndi chitenje.

“Koma pambalipa adasiya kalata yomwe adalembera mphunzitsi wamkulu wa pasukulu ya pulaimale ya Munthelele yowatsanzika kuti sapitiriza sukulu chifukwa moyo wake watha,” Dumbulira adatero.

Iye adati kudzikhweza kukukula m’deralo koma samayembekezera kuti mwanayo angalimbe mtima motere chifukwa adali wanzeru komanso wolimbikira pa maphunziro.

Naye mneneri wa polisi m’boma la Nkhata Bay Ignatius Esau adatsimikiza za imfayo.

“Ndi zoona kuti mwana wa zaka 15 wadzikhweza ku Bula ndipo nawo achipatala atsimikiza kuti adadzipha kaamba kodzimangirira,” adatero Esau.

Nkhani zodzikhweza zikuchulukira-chulukira m’dziko muno, ndipo masiku apitawa apolisi adati amuna ndiwo akudziphedwa kwambiri kuposa akazi. n

Related Articles

Back to top button