Chichewa

Adzikonzera ‘mpumulo wa bata’

Listen to this article

 

Ukayenda umaona agalu a michombo ndithu. Ku Rumphi aliko oyenda masanasana pamene bambo wina wa zaka 62 wakumbiratu manda owaka bwino kuyembekezera tsiku lomwe Namalenga adzati kwatha.

Sasintha Mnozga, yemwe ndi mbusa wa mpingo wa African Church adakonza mandawa ndi ndalama zoposa K200 000 m’mudzi mwa Mnozga, mfumu yaikulu Chikulamayembe m’bomalo.

Koma mafumu m’derali ndi wodabwa ndi mchitidwewu, zomwe akuti ndi zotsutsana ndi chikhalidwe cha Atumbuka pakuti munthu saloledwa kukumbiratu manda ake.

‘Mandawo’ ndi amenewa: Pali tsiku lakubadwa koma palibe lakufa
‘Mandawo’ ndi amenewa: Pali tsiku lakubadwa koma palibe lakufa

Mnozga, pocheza ndi Msangulutso Lachitatu, adati sakuonapo vuto lililonse mwakuti pano akusakasaka makobidi ena kuti aguliretu bokosi lomwe adzamuyikemo akamwalira.

“Ndikufuna kukonzeratu zonse kuti abale anga asadzavutike kusakasaka makobidi okonzera manda anga ndikadzamwalira. Abale anga ambiri ndi ovutika moti sangadzakwanitse kugula ngakhale bokosi,” adatero Mnozga yemwe ali ndi ana 10.

Iye adati china chomwe chidamuchititsa kuti akumbiretu manda ndi momwe anthu salemekezera maliro kumanda.

“Anthu amangoponya dothi pamwamba pabokosi ngakhale litakhala la makobidi ochuluka bwanji. Izi sizimandisangalatsa konse.

“Mandawa ndawakonza ndi miyala komanso matumba 11 a simenti. Izi zikutanthauza kuti bokosi langa silidzakhunzana ndi dothi monga mmene zimakhalira m’manda ena,” adatero Mnozga.

Mnozga amachitanso bizinesi pa boma la Rumphi. Ali ndi chigayo komanso malo ogonapo alendo. Iye adali mfumu kumudzi kwawo koma adasiyira mwana wawo atayamba ubusa m’chaka cha 2001.

Pamene adayamba kukumba mandawa m’chaka cha 2013, abale awo adawakaniza koma iwo adakakamirabe. “Poyamba ankakana koma nditawalongosolera chifukwa chomwe ndimachitira izi adavomera mosasangalala momwemo.

“Koma kwa mafumu silidali vuto chifukwa adali anzanga paja nane ndidali mfumu,” adatero Mnozga.

Mfumu yaikulu Chikulamayembe, yomwe idati idawaonapo mandawa, idakana kulankhulapo pankhaniyo.

Koma mfumu Kayiwale Chirambo ya m’derali idati zomwe adachita Mnozga sizololedwa pa chikhalidwe chawo.

“Pachikhalidwe chathu sitivomera munthu kukumbiratu manda ake. Koma vuto ndi lakuti masiku ano anthu ali ndi ufulu ochita zomwe akufuna. Pachifukwa ichi, mpovuta kuti timuletse,” adatero a Chirambo.

Iye adati sakudziwa chomwe chidachititsa Mnozga kubwera ndi ganizo lotereli.

“Ife sitikudziwa kuti kaya ndi misala, kaya ndi uKhristu kapena chuma. Tonse ndife odabwa, koma palibe chomwe tingachitepo chifukwa chakuti ndi ufulu wake kutero.

“Koma kukanakhala kwakale tikadawaitanasa nkuwaletsa kuchita zimenezi. Atati akana tikadatha kuwalanga,” adatero Chirambo.

Mnozga siwoyamba kudzikumbira manda m’bomali. Pa Mzokoto padalinso a SS Ng’oma yemwenso adazikumbira manda. Koma atamwalira abale awo adakhaniza zokawayika kwina ndi komwe adamanga mandawo.

Asanamwalire, mtsogoleri wakale wa dziko lino Bingu wa Mutharika adakonzeratu nyumba yomaliza yomwe adagonamo iye ndi mkazi wake Ethel. Mandawo amatchedwa Mpumulo wa Bata.

Padakalipano, anthu ku Rumphi ali ndi chidwi kuti kufuna kudziwa kuti Mnozga adzasungidwa kuti akadzamwalira. n

Related Articles

Back to top button