Chichewa

Adzinjata Kaamba Ka Mkazi Wamwini

Listen to this article

 

Chisoni chidaphetsa nkhwali. Ku Masasa, mumzinda wa Mzuzu mnyamata yemwe adalembedwa ntchito ya zomangamanga pakhomo pa bambo wina m’derali mongomuthandiza atamumvera chisoni kaamba ka kuvutika, akumuganizira kuti adapezeka akuzemberana ndi mkazi wa njondayo.

Koma zachisoni-nkhaniyi akuti yatengera Joseph Nyirongo, yemwe adali wa zaka 23, kumanda atapezeka ali lende mumtengo wa paini pambuyo pomupezerera akuchita zadama m’nyumba mwake ndi mkazi wa njondayo.

Nyamhone: Nachi chitsa cha mtengo wotembereredwa, pomwe adadzimangirira mwana wanga
Nyamhone: Nachi chitsa cha mtengo wotembereredwa, pomwe adadzimangirira mwana wanga

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi m’chigawo cha kumpoto, Cecilia Mfune, watsimikiza za nkhaniyi.

Mkati mwa sabatayi Msangulutso udacheza ndi mwini mkaziyo, Lovemore Luhanga, yemwe adanenetsa wamukhululukira atchalitchi atamukhazika pansi ndipo wati samusiya mkazi wake.

Luhanga, yemwe amaoneka mosatekeseka ndi mbiri yomwe yatchuka m’derali, adati zili kwa mkazi wakeyu kusintha kapena ayi ati kaamba koti zomwe adachita zapangitsa munthu wina kuluza moyo wake.

“Koma pachikhalidwe ndiwatumiza kaye kumudzi kuti akapitidwe mphepo yabwino; adzachita kubweranso,” Luhanga adatero.

Bamboyu adati panthawi yodzikhwezayo Nyirongo adali atavala scumba ya akazi ake ya mtundu pepo (purple).

“Mwana wanga wa zaka zitatu ndiye adaizindikira scumbayo chifukwa adapita ndi mnzake wa zaka 8 kukaona thupilo lili mumtengo ndipo adayamba kulozera mnzakeyo kuti amvekere ‘amama bafwa, bali muchikhuni’ ataona scumbayo,” Luhanga adatero.

Polongosola chomwe chidatsitsa dzaye, iye adati adayamba kumva mphekesera kuti mkazi wake akuzemberana ndi mnyamatayu mwezi wa November chaka chatha.

Luhanga, yemwe amachita bizinesi komanso ndi diraiva wa lole, adati mkazi wake wakhala akukana za chibwenzichi.

“Amati sangachite naye chibwenzi chifukwa Nyirongo sankasamba; ndipo nanenso ndimakaikira chifukwadi adalibe ukhondo,” iye adatero.

Koma Luhanga adati chibwenzichi chitafumbira, mkazi wakeyu adamupezera nyumba mnyamatayo komanso adayamba kumamupatsa ndalama zomwe amakatolera kubizinesi yawo yoperekera sopo wochapira ndi mafuta odzola.

Bamboyu adati Lachiwiri sabata yapitayo adalimba mtima ndi kumufunsa Nyirongo za mphekeserazo, zomwe ati mnyamatayo adakanitsitsa kwa mtu wa galu kuti sakudziwapo kanthu.

“Apa akazi anga adatulukira ndipo nawonso adakanitsitsa za nkhaniyi. Ndidangowauza kuti ngati akuchitadi izi, tsiku la fote lidzawakwanira ndipo chomwe chitadzachitike sindidzalankhula zambiri. Tili mkati mokamba mayi anga adatulukira kudzatichezera ndipo nkhaniyi idathera pomwepo,” adafotokoza motero Luhanga.

Iye adati patadutsa nthawi adatengana ndi mkazi wake komanso mwana wawo wa zaka zitatu kuwaperekeza mayi ake; koma mwadzidzidzi adazindikira kuti mkazi wake sali nawo paulendowu ndipo sikudziwika komwe alowera.

Luhanga adati adachoka koperekeza mayi ake nthawi ili cha m’ma 9 koloko usiku adatsekera ana m’nyumba ndi kuyamba kufufuza komwe mkazi wakeyo adalowera chifukwa adali ndi K43 000 yomwe adatolera tsiku limenelo.

Iye adati nthawi ili cha m’ma 1 koloko mmawa anthu ena adamutsina khutu kuti mkazi wakeyo akamuyang’ane kunyumba kwa Nyirongo.

“Nditafika ndidaima pawindo ndipo ndidamva awiriwo akulankhula. Apa ndidadzutsa eni nyumbazo kuti andikhalire umboni. Ndipo titagogoda, Nyirongo adatitsekulira koma adakanitsitsa zoti mkazi wanga adali m’nyumbamo,” Luhanga adalongosola motero.

Bamboyo adati adamulonjeza Nyirongo kuti ampatsa K10 000 ngati mkazi wakeyo sadali m’nyumbamo.

“Adanditsekulira ndipo nditangoti lowu, adandiponyera chikwanje pamutu chomwe chidandiphonya ndi kumenya feremu ya chitseko, kenaka adandimenya ndi chitsulo padiso ndi pamutu ndipo ndidagwa pansi. Apa nkuti mkazi wanga atathawira pawindo,” bamboyo adatero.

Iye adati atadzuka adakuwa kuti: “Wakuba! Wakuba!” ndipo anthu ozungulira adamugwira mkaziyo n’kuyamba kum’menya.

Iye adati adaleretsa mkazi wakeyo m’manja mwa anthu okwiyawo ali buno bwamuswe ndipo adamupititsa kupolisi achisoni atamuponyera kachitenje. Luhanga adati adatengera mkazi wake kupolisiko pomuganizira kuti waba ndalama kaamba koti ndalama yomwe adali atatolerayo adali atamupatsa Nyirongo “poti awiriwo amakonzekera zothawira ku Lilongwe”.

“Ndidatengana ndi apolisi kuti tidzamutenge Nyirongo, koma sitidamupeze. Ndidadzidzimuka kumva kuti wapezeka atadzimangirira,” adatero Luhanga.

Pakadalipano mkaziyu akubindikira m’nyumba kaamba ka manyazi ndi zomwe zidachitikazi chifukwa akatuluka anthu amangomulozaloza. Adakana kutuluka kuchipinda pomwe Msangulutso udafuna kumva mbali yake.

Mkucheza kwathu ndi mayi a wodzikhwezayo, mayi Nyamhone, iwo adati adazindikira kuti mwana wawoyo adadzimangilira nthawi ili m’ma 4 kololo mmawa wa Lachitatu ndipo sadasiye uthenga uliwonse.

A Nyamhone, omwe amagulitsa masuku, adati anzake ndi amene adawauza kuti mtengo womwe uli pafupi ndi nyumba yawo mukulendewera munthu.

Mayiwo adati mwana wawoyo, yemwe wasiya ana awiri ndipo banja lake lidatha m’chaka cha 2010, adadzamugogodera cha pakati pa usiku ati kukangowaona.

Nyamhone adati Nyirongo adadzimangirira mumtengo wautali kwambiri ndipo pa nthawi yomwe adamuonayo adali asanamalizike koma kuti anthu sadakwanitse kukwera kuti amuombole.

“Mwana wanga sadayambane ndi munthu aliyense ndipo sadandilongosolere kalikonse zokhudza mzimayi,” a Nyamhone adatero.

Iwo adati koma adali okhumudwa ndi apolisi omwe ngakhale adauzidwa za ngoziyo mmawa adafika pamalopo 12 koloko masana ndipo thupilo sadalitengerenso kuchipatala ati kaamba koti lidali litayamba kale kufufuma.

Koma wachiwiri kwa mneneri wa polisi m’chigawochi watsutsa zoti thupi la Nyirongo sadalitengere kuchipatala kuti akayeze gwero la imfa. Mfumu ya derali yomwe tidacheza nayo idatsimikiza kuti maliro sadapitedi kuchipatala monga akunenera apolisi. n

 

 

Related Articles

Back to top button