Chichewa

Afa atamwa bibida wosadyera

Listen to this article

 

Mneneri wa polisi ya Nkhotakota Williams Kaponda watsimikiza kuti bambo wina kumeneko wakabzala chinangwa atapapira mowa osadyera.

Kaponda adati malinga ndi achibale, Damson Wasiya, 34, malemuwo omwe ndi Francis Phiri adapita kukapopa mowawo Lamulungu pa 8 November m’bomalo.

Achibalewo auza apolisi kuti malemuwa adapezeka usiku akuchokera kopopa mowawo ali lamba! Mumsewu, zomwe zidakhudza ofuka kwabwino amene adamutengera kunyumba.

“Ataona kuti mbaleyo akuoneka moti samapeza bwino, adathamangira naye kuchipatala cha boma komwe madotolo adakatsimikiza kuti adali atafa,” adatero Kaponda yemwe adati zotsatira za achipatala zidaonetsa kuti malemuwo adafa chifukwa chomwa wosadyera.

Malemuwa omwe adali ndi zaka 47 amachokera m’mudzi mwa Sasani kwa T/A Malengachanzi m’bomalo.n

Related Articles

Back to top button
Translate »