Chichewa

Afisi a ku ntcheu abwereranso?

 

MAyi adaphedwa, ana ake anayi ndi mlamu wake adavulazidwa. Pano ziweto 10 zagwidwa m’midzi 14 ya mwa T/A Phambala m’boma la Ntcheu.

Alenje aboma amene adapitako kukasaka afisiwa, adangokhalako masiku atatu ndi kuchokako, lero anthu agwidwa ndi mantha.

Mkulu woona nyama za kuthengo ndi nkhalango Bright Kumchedwa adati nkhaniyi adaimva ndipo lipoti la momwe alenjewo adayendera lidatumizidwa.

Harrison Lano, mmodzi mwa olumidwa ndi fisi m’chipatala

“Tikukonza zoti tibwererenso kumudziko. Chomwe tikuyang’ana panopa ndi ndalama. Zonse zikatheka, tibwerera konko,” adatero Kumchedwa.

Koma iye adati anthu aleke kuyenda usiku komanso asalole kuti ana aziyenda okha kuopa ngozi.

Kodi afisi a ku Ntcheu amene adatchuka m’zaka za m’ma 1990 ayambiranso? Ili ndiye funso la anthu a m’bomali.

Bambo wa ana ovulazidwawa akuti moyo wawo uli pachiswe ndipo boma likuyenera lichite kanthu kupulumutsa anthuwa.

Bamboyu, Alfred Thala, wa m’mudzi mwa Thala akuti chivulazireni ana ake ndi kupha mkazi wake, anthu akukhala mobisala.

“Pano akumayenda m’magulu, tsiku lililonse afisi akumamveka akulira kuyambira cha m’ma 5. Tili ndi mantha kuti tsiku lililonse tingaonenso ngozi ngati yomwe idachitika,” adatero Thala.

Iye adati chiphereni mkazi wake pa 2 December chaka chino, mudzi wawo mwagwidwa ziweto 6.

“Sabata yatha yomweyi adzagwira nkhumba kunyumba kwanga. Mbuzi agwira mwa anthu ena m’mudzi momwemu. Komanso mudzi woyandikana ndi ife agwira mbuzi zinayi.

“Akumafika pakhomo, sungatulukenso kuopa kuti akugwira, uwu ndiye ukumakhala mwayi wawo kuti agwire ziweto,” adatero Thala.

Ngoziyo itachitika, alenje a boma adafikako koma adangokhala masiku atatu n’kuchokako zomwe sizidakomere anthu akumeneko.

“Tsiku lililonse afisi amadutsa koma sadaphe ngakhale fisi mmodzi mpaka adapita. Tidawauza kuti asachoke koma sadamvere ndipo adapita,” adatero Thala.

DC wa boma la Ntcheu Paul Kalilombe adati nkhaniyi adaimvanso moti panopa akukambirana ndi oyang’anira za nkhalango ndi nyama zakuthengo kuti athandize.

“Nkhani yoti afisi avuta kuno tidaimva ndipo tikulumikizana ndi alenje kuti atithandize,” adatero Kalilombe.

Koma Senior Chief Kwataine ya m’bomali yati ngakhale afisiwa avuta, anthu asaganize kuti afisi amene adatchuka padzana abwereranso.

“Afisi a nthawi imene ija adali odabwitsa chifukwa amayenda masana. Amakhoza kufika pamaliro n’kugwira munthu.  Amene aja adapita chifukwa zimaonetsa kuti akuchokera ku Mozambique. Afisi awawa kulipo akuchoka,” adatero Kwataine.

Komabe Thala akupenekera kuti alipo akufuna kuwachita chipongwe anthu a midzi yawo.

“Alenje amatchera mfuti, amaikapo nyama kuti adye, upeza angodya nyama inayo koma nyama yomwe yayandikira kotulukira zipolopolo samadya. Awa ndi afisi enieni? Ndikukaikira.

“Afisi enieni amathawa anthu komanso amayenda usiku wokhawokha dzuwa likalowa, koma awawa akudabwitsa chifukwa akuyenda masana,” adaonjeza.

Midzi yomwe afisiwa avuta ndi Thala, Kumkeyani, Chingeni, Masiku, Ntsitsamwaye, Chigumbu, Kamodzi, Matchereza, Nachakwa, Javelo, Musa, Mpochela, Gangawako, Mandaadona ndi ina. n

Related Articles

Back to top button