Nkhani

Afuna chitukuko chofanana m’madera a aphungu

 

Ntchito za chitukuko m’madera oyimiriridwa ndi aphungu a ku Nyumba ya Malamulo chiyamba kufanana tsopano ntchito yodulanso malire ikachitika.

Bungwe loyang’anira zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lati ntchitoyi tsopano ikungodikira katswiri wochokera kunja yemwe adzaigwire.Kalenge-Bridge

“Zonse zatheka tsopano tikungodikira katswiri yemwe achokere kunja kudzagwira ntchito yodulanso malirewa. Katswiriyu sitikumudziwa koma atumizidwa ndi akuluakulu a bungwe la Commonwealth,” chidatero chikalata chomwe bungweli lidatulutsa.

Mneneri wa bungwe la sisankho m’dziko muno, Sangwani Mwafulirwa, adati kudulanso malirewa kuthandiza kuti aphungu onse 193 azikhala ndi madera ofanana komanso chiwerengero chofanana cha anthu.

“Madera ena pakalipano ndi aakulu kwambiri pomwe ena ndi aang’ono kwambiri ndiye poti aphungu amagwira ntchito imodzi, tikufuna kuti madera awo akhale ofanana kuti ntchito ikhalenso chimodzimodzi,” adatero Mwafulirwa.

Iye adati mwachitsanzo dera la chigawo cha pakati m’boma la Lilongwe ndicho chili chachikulu kwambiri ndi anthu oponya voti 126 115 pomwe dera la chilumba cha Likoma ndicho chochepetsetsa ndi anthu ovota 6 933 basi.

Ngakhale pali kusiyana kotereku ndalama za chitukuko zomwe aphungu amalandira zotukulira madera awo zimakhala chimodzimodzi kutanthauza kuti ndalama zomwezo kwina zikuthandiza anthu ochuluka kuposa kwina.

Ngakhale zinthu zili choncho, palinso nkhani yosintha ndondomeko ya kayendetsedwe ka chisankho yomwe kauniuni wa malamulo akale adachitika ndipo komiti yomwe imachita kauniuniyu idatulutsa kale zotsatira zake.

Imodzi mwa mfundo zikuluzikulu m’ndondomeko yatsopanoyi ndi yakuti aphungu asamakhale ndi malire koma kuti boma lililonse lizikhala ndi chiwerengero cha aphungu potengera chiwerengero cha anthu mbomalo.

Mwafulirwa adati bungwe la MEC silinganenepo kanthu pa za tsogolo la ntchito yodulanso madera a aphungu potengera malamulo atsopanowa pokhapokha nthambi ya zamalamulo idzanene mfundo yomaliza.

“Nzoonadi, ndondomeko yatsopanoyi idapangidwa koma sidaperekedwe kunthambi ya zamalamulo (Law Commission). Zonse zidzidziwika nthambiyi ikadzanena maganizo ake. Panopa tiyeni tibatsata zomwe zilipo,” adatero Mwafulirwa.

Related Articles

Back to top button