Nkhani

Agona ku maofesi a khonsolo ya Mzuzu

Listen to this article

Mayi wina yemwe ndi mlembi kunthambi yoyang’anira za umoyo pakhonsolo ya mzinda wa Mzuzu, anadabwitsa anthu masiku apitawa pomwe anasamukira paofesi ya bwanamkubwa wa khonsoloyo chifukwa wakhala osalandira malipiro ake kwa miyezi iwiri. 

Ndinawe Mtambo wa zaka 28 anagona panja pa maofesi a khonsoloyo kwa masiku awiri.

Katundu wa a Mtambo adali kuseri kwa ofesi za khonsolo

Pakhondepo, mayiyo anaika firiji, bedi loyala bwino komanso akatundu ena pokakamiza kuti khonsoloyo ikonze mavuto a za chuma omwe yakhala ikukumana nawo kuchoka m’chaka cha 2017.

“Ndikudandaula chifukwa anandichotsapo msanga. Ndimafuna ndizikhala pompo mpaka unduna wa maboma aang’ono komanso mtsogoleri wa dziko lino alowererepo,” anatero a Mtambo.

Polankhula ndi Msangulutso, iwo adati a khonsoloyo anakawatenga mayi awo ndi omwe anadzachotsa katunduyo.

A Mtambo adaonjezeranso kuti akhonsoloyo adatuma munthu wawo kuti amutengere kuchipatala cha amisala kuti akamuyeze.

“Akuofesi anapitanso kwa mayi anga kukawapempha kuti awapatse chilolezo chonditengera kuchipatala cha amisala koma ndinawakanira chifukwa kuchipatala sakakamizana,” adatero iwo.

Iwo adati a khonsoloyo adawapatsa malipiro awo a miyezi iwiri atatha masiku awiri akugona panjapo.

“Nditangoyamba kugona panja anthu ena amandinena kuti ndili ndi mavuto pomwe ena anandisilira ndipo ankafuna kuchita ngati ine koma ndidawakaniza chifukwa zomwe ndinachitazo zinali za ukadziotche,” analongosola motero a Mtambo.

Iwo adati panthawiyo ankalawilira m’mawa n’kukasamba paseli pa maofesiwo pomwe chakudya amaphikanso pomwe panali katundu wawo.

Apa anaonjezera kuti ngati zinthu sizisintha pakhonsoloyo adzachitanso za mtunduwo koma zagulu lalikulu osati zayekha.

“Ndikukhulupilira kuti uthenga wa mavuto omwe tikukumana nawo wafika tsopano ndipo papezeka njira zowathetsera,” anatero a Mtambo.

Iwo anati chodandaulitsa kwambiri n’choti ngakhale mabungwe okongoza anthu ndalama akumawasala akangomva kuti amagwira ntchito kukhonsolo ya mzinda wa Mzuzu ndipo sakumawapatsa ngongole.

Mavuto a zachuma afika posauzana pa khonsoloyo chifukwa pomwe Msangulutso umacheza ndi a Mtambo muofesi yake, kunafikanso amayi ena wogwira ntchito pamalopo omwe anadandaulanso kuti alibe kalikonse.

Ogwira ntchito ena pa khonsoloyo ati akhala miyezi isanu osalandira malipiro awo.

Mneneri wa khonsolo ya Mzuzu a Macdonald Gondwe anatsimikiza kuti a Mtambo anayamba kugona panja Loweruka ndipo akhonsolo anampatsa malipiro ake a miyezi iwiri Lamulungu.

“Anayamba kugona kuno Loweruka, tinampatsa malipiro ake m’mawa wa Lamulungu, koma chodabwitsa n’choti madzulo a tsiku lomwelo anapitanso kwawo kukatenga katundu woonjezera monga firiji ndi zofunda komanso zofunda,” analongosola a Gondwe.

Malinga ndi a Gondwe aliyense ndi wodabwa paofesipo chifukwa Mtambo sanachiteko zimenezi. A Gondwe anatsimikizanso kuti ngakhale a khonsolo anapempha kwa mayi ake kuti a Mtambo apite kuchipatala, izi sizinachitike.

Related Articles

Back to top button
Translate »