Chichewa

Agulitsa chimanga kudziko la tanzania

Listen to this article

 

Pomwe boma lili pakalikiriki kuitanitsa chimanga kuchokera kunja pofuna kupulumutsa Amalawi ku galu wakuda yemwe wadutsa madera ambiri m’dziko muno kaamba ka kuchepa kwa mvula chaka chatha, zamveka kuti Amalawi ena agundika kugulitsa chimanga chawo kudziko la Tanzania.

Themba la Mathemba (Paramount Chief) Chikulamayembe ya m’boma la Rumphi yauza Tamvani, kuti alimi ambiri m’dera lake agulitsa chimanga chawo mozemba kumavenda ochokera m’dziko la Tanzania mmalo mogulitsa kumisika ya Admarc.

Iye adati izi zikuchitika ngakhale ena mwa anthu ake ali pachiopsezo chachikulu chokulukutika ndi njala.

Chikulamayembe: Kulankhula ndiye tikulankhula koma ena samamva
Chikulamayembe: Kulankhula ndiye tikulankhula koma ena samamva

“Chimanga chidachitako bwino pang’ono chigawo cha kumpoto,kuphatikizapo boma la Rumphi, koma makomo ambiri avutikabe ndi njala. Izi zili chomwechi chifukwa chimanga chambiri chalowa m’dziko la Tanzania,” adatero Chikulamayembe.

Mfumuyi idati kumbali yake ikuyesetsa kuchititsa misonkhano kuuza anthu za kuipa kogulitsa chimanga kunja pomwe m’dziko muno muli njala yadzaoneni.

“Ambiri akumvetsa, koma ena amakopekabe ndi mitengo yokwera yomwe mavenda akunjawa amapereka powagula poyerekeza ndi ya Admarc koma amaiwala kuti nthawi yanjala adzagulanso chimanga chomwecho kwa mavenda omwewo pamtengo wokwera kwambiri,” adatero Chikulamayembe.

Iye adapempha boma kuti lichitepo kanthu pokhwimitsa chitetezo m’malire a dziko lino ndi maiko oyandikana nawo kuti chimanga chosowachi chisamatuluke chisawawa.

Pakalipano, boma la Malawi layambapo kuitanitsa chimanga kuchokera kumaiko ena monga ku Brazil, Ukraine, Mexico ndipo china chayamba kale kulowa m’dziko muno kuchokera ku Zambia.

Anthu oposa 6.5 miliyoni m’dziko muno alibiretu chakudya moti akufunika thandizo mwachangu, malinga ndi lipoti la Malawi Vulnerability Assessment Committee (Mvac).

Powunikira izi, ndondomeko ya zachuma ya dziko lino idaika padera ndalama zokwana K35 biliyoni zogulira chimanga m’dziko muno komanso kumaiko akunja chokwana pafupifupi matani 1 miliyoni choti anthu adzadye njala ikafika posauzana.

Chanda Kasolo, mmodzi mwa akuluakulu omwe ali mukomiti ya pulezidenti wa dziko la Zambia yoyang’anira chimanga ndi zina zotere lotchedwa Presidential Multi-Agency Taskforce on Maize, Maize Products and Food Security, adatsimikiza kuti dziko lino lidaitanitsadi chimanga chopitirira matani 500 000, ndipo matani 150 000, adatumizidwa kale sabata zitatu zapitazo.

Iye adati chimangachi chikugulidwa pamtengo wa pafupifupi $15 (MK11 250) pathumba la makilogalamu 50 lililonse.

Koma pomwe ena ku Rumphi akugulitsa chimanga kwa mavenda a ku Tanzania, Lachinayi sabata yatha boma la Zambia lidalanda matani 90 a chimanga kudzanso matani 30 a ufa omwe ena amafuna kulowetsa m’dziko muno mozembetsa. Mu April dzikolo lidagwiranso galimoto zikuluzikulu 28 zitanyamula chimanga chomwe amafuna kulowa nacho m’dziko muno mosatsata ndondomeko.

Kasolo adati Amalawi asabwekere chimanga cholowa m’dziko muno mozembetsedwa chifukwa chikumagulitsidwa pamtengo wodula kwambiri.

“Akumachigula pamtengo wa K80 ya Zambia (yomwe ndi pafupifupi K5 678 ya Malawi) ndipo akuchigulitsa mokwera kwambiri kwa Amalawi m’boma la Mchinji,” adatero Kasolo.

Iye adati boma la Zambialo ndi lokhumudwa ndi mchitidwewu chifukwa ukulowetsa pansi chuma cha maiko awiriwa.

Pokambapo za mmene zilili m’dziko muno, Symon Vuwa Kaunda, mmodzi wa alangizi a pulezidenti wa dziko lino, adauza atolankhani kuti chigawo chakumpoto, makamaka boma la Mzimba, kuli chimanga chambiri zedi chomwe bungwe logula ndi kugulitsa mbewu kwa alimi la Agriculture Development and Marketing Corporation (Admarc) silitha kugula  chonse.

Koma Kaunda adangoti kakasi, kukaninka kuyankha atamufunsidwa kuti n’chifukwa chiyani boma likulimbana ndi chimanga chakunja pomwe likukanika kugula chimanga chamnanu chomwe iye akuti chilipo m’boma la Mzimba.

Ndipo zidali zamanyazi pomwe atolankhani adafika ku depoti ya Admarc mumzinda wa Mzuzu komwe adapezako matani 2 800 okha. Malowa amadzadza ndi matani 10 000.

Kafukufuku wa Mvac adati boma la Mzimba ndi limodzi mwa maboma omwe akhudzidwe ndi njala mwa anthu 12 pa 100 alionse pomwe anthu 16 pa 100 alionse avutika ndi njala m’boma la Rumphi.

Koma mavuto aakulu ali m’maboma a Nsanje ndi Chikwawa komwe, malinga ndi lipoti la Mvac, pafupifupi anthu 90 pa 100 alionse alibiretu chakudya moti ngati slandira thandizo la chakudya msanga ambiri afa ndi njala.

Maboma ena komwe galu wakuda wavuta kwambiri ndi Balaka, Blantyre, Zomba, Machinga, Mangochi ndi Thyolo m’chigawo cha kummwera.

Chokhumudwitsa kwambiri n’chakuti mbewu zina monga chinangwa, mbatata ya kholowa ndi kachewere kudzanso mapira, zomwe anthu amapulumukirapo chimanga chikalephereka, nazonso sizidachite bwino kaamba ka chilala.

Ali ndi mwana agwiritse-chaka chino ngati thumba la chimanga la makilogalamu 50 silifika K25 000 ndi mwayi, tikatengera kuti chaka chatha thumba lidali pakati pa K10 000 ndi K15 000 madera ambiri. (Zoonjezera: Joseph—Claude Simwaka) n

Related Articles

Back to top button
Translate »