Chichewa

Agumula nyumba pokaikira masalamusi

Listen to this article

Mbuto ya kalulu idakula ntadzaonani.  Mwambiwu udapherezera Lachiwiri ku Lilongwe pomwe anthu okwiya ku Mtsiriza adagumula nyumba ya banja lina ati powaganizira kuti amazembetsa anthu m’matsenga.

Anthuwo sadalekere pomwepo, koma kuotcha galimoto lapolisi lomwe apolisi adakwera kuti akateteze banja la Malunga amene adaotcheredwa nyumbayo.

Mneneri wa likulu la apolisi James Kadadzera watsimikiza za chipolowecho ndipo wati apolisi agwira anthu 20 omwe akuwaganizira kuti akukhudzidwa pa chipolowecho.

Kadadzera: Tilibe lipoti

“Awa tawagwira ngati poyambira kafukufuku ofuna kupeza chenicheni chomwe chidachitika chifukwa pakumveka nkhani zosiyanasiyana ngakhale mphekesera yaikulu ikukhudza za masilamusi,” adatero iye.

Polankhula ndi Msangulutso, anthu omwe adaona izi zikuchitika adati banjalo amalikaikira kuti limasowetsa anthu mmatsenga ndipo patsikulo, munthu wina yemwe amalira momvetsa chisoni adawauza kuti Mulungu

adamuonetsa vumbulutso akupephera kuti mbale wake yemwe adasowa akusungidwa m’nyumbamo.

Mmodzi mwa anthuwo, Enifa Kaira, adati mphekeserayo itamveka anthu adayamba kusonkhana panyumbapo uku akukalipa kuti eni nyumbayo atulutse anthu onse omwe amawasunga m’matsenga.

“Kudali khamu la anthu: Ana, akulu ndi okalamba kufuna kuonetsetsa kuti m’nyumbamo mutuluka chiyani. Eni nyumbayo ataona kuti zinthu zikuonjeza, adamuuza odandaulayo kuti alowe m’nyumbamo akayang’ane mbale wakeyo koma naye sadatuluke mpaka apolisi adafika,” adatero iye.

Kaira adati apolisi atafika adathamangira m’nyumbamo ndipo potuluka adatenga odandaulayo ndi eni nyumbayo n’kuwakweza galimoto ya polisi kuti azipita nawo koma anthu sadakondwe nazo ndipo adayamba kugenda apolisiwo nkuwayatsira galimotoyo.

Mwana wamkulu wa m’nyumbamo Mwayi Malunga, wa zaka 24, yemwe adali pakhomo pomwe izi zimachitika adati zomwe anthuwo adachita lidali dumbo chabe poti anthu m’deralo safunira banjalo zabwino.

Iye adati pomwe zonse zidayamba m’ma 3 koloko masana iye akupuma ndipo amamvera phokoso la anthu kutulo osadziwa kuti kukuchitika chiyani mpaka pomwe mayi ake adamudzutsa kuti akaone zomwe zikuchitika kunja.

Malunga adati atatuluka panja adaona khamu la anthu likusokosa uku likuloza nyumbayo pakati pawo pali munthu wa mtsikana akulira uku akuti akufuna mbale wake yemwe ali m’nyumbamo.

“Pokana milandu, tidamupatsa mwayi woti alowe m’nyumbamo ayang’ane paliponse ndipo adafufuzadi koma osapeza kanthu kenako tidangoona wagwa nkukhala ngati wakomoka mpaka pomwe apolisi amafika,” adatero Malunga.

Iye adati apolisiwo akuti azinyamuka ndi munthuyo komanso makolo ake, anthu adayamba kuwakuwiza kenako kugenda koma apolisiwo adaliza galimoto yawo ndipo asadafike patali, anthuwo adayiyatsa iwo nkuthawa.

Mnyamatayo adati anthuwo adayamba kugenda nyumba yawo mpaka kuswa magalasi onse, chitseko komanso ena adakanganula malata mbali imodzi nkugwetsa mpanda wa njerwa komanso kuzula chitseko cha mpandawo nkunyamula.

“Zidali zachidziwikire kuti kwinako zidalowa kuba basi osati zomwe amanenazo chifukwa mpaka pano munthu yemwe amati tikusungayo sadamupeze,” adatero iye.

Kadadzera adati chodabwitsa nchakuti apolisi alibe lipoti lokhudza munthu yemwe akuti adasowayo komanso atachita chipikisheni m’nyumbamo sadapezemo munthu wosonyeza kuti amasungidwa mobedwa.

Iye adati apolisi ndiwokhudzidwa kuti mchitidwe woweruza potengera mphekesera ukukula ndipo adati nkulakwitsa kutengera lamulo mwaokha mokanena kupolisi komwe kuli ndondomeko zofufuzira ndi kutengera oganiziridwa kulakwa kubwalo la milandu.  n

Related Articles

Back to top button
Translate »