Chichewa

Agwiriridwa ali mtulo

Pali zina zikamachitika, sungamvetse kuti zakhala bwanji. Mtsikana wina wa zaka 18 yemwe ali pabanja wagwiriridwa ali mtulo kumalo owedzera nsomba a Khuni, ku Dwangwa, m’boma la Nkhotakota.

Mtsikanayu adagwiriridwa pomwe naye mwamuna wake adali mtulo tofa nato pambali pake.

“Ndinkalota ndi kugona ndi munthu, ndipo nditadzidzimuka, ndidapezadi kuti ndikugona ndi munthu,” mtsikanayu adauza bwalo la milandu la

Nkhunga, m’bomalo.

Mtsikanayo akuti ankaganiza kuti munthuyo adali mwamuna wake koma adadabwa atanunkhiza mowa ndipo adazindikira kuti ankagwiriridwa chifukwa mwamuna wake samwa mowa komanso apa ndi pomwe adaona kuti mwamuna wake adali mtulo tofa nato pambali pake.

Apatu mpomwe adakuwa ndipo anthu adamugwira wogwirirayo ndi kupita naye kupolisi komwe adamutsekulira mlandu wogwiririra mosemphana ndi gawo 133 la malamulo a dziko lino.

Polankhulapo, mneneri wa polisi ya Khunga, Ignatius Esau adati udali usiku wa pa 16 August pomwe Raphael Kasakula wa zaka 21, adakalowera

m’nyumba banjalo   ndi kugwirira mayi wa m’nyumbamo.

Esau adati Kasakula yemwe ali ndi mkazi komanso ana awiri adauza bwalo la milandu la Nkhunga Lachisanu sabata yatha kuti mowa ndi omwe udamuchimwitsa.

“Kafukufuku wathu ngati apolisi udaonetsa kuti padalibe ubwenzi ulionse wa mseri pakati pa awiriwo koma kuti Kasakula adali mnzake wa mwamuna wa mtsikana yemwe adamugwirirayo,” adatero Esau.

Iye adati, koma anthu adadabwa kuti nkhaniyi ili ku bwalo la milandu, banjalo lomwe ndi asodzi, lidapempha a bwalo kuti atseke mlanduwu chifukwa Kasakula ndi mnzawo.

Koma woweruza milandu pakhotilo, Kingsley Buleya, adampeza Kasakula wolakwa pamlandu wogwiririra ndipo adamugamula kukakhala kundende kwa zaka 6.

Related Articles

Back to top button