Chichewa

Agwiririra ndi kupha gogo

Listen to this article

 

Pomwe dziko lapansi likukumbukira tsiku la amayi pamutu woti ‘Kuthetsa Nkhanza kwa Amayi ndi Ana’, anthu achiwembu ku Mchinji adagwiririra ndi kupha gogo Vigilita Sakala, wa zaka 61, n’kumutaya mmphepete mwa munda wake.

Mneneri wa polisi m’bomalo, Moses Nyirenda, watsimikiza za nkhaniyi koma wati anthu omwe adachita chiwembucho sadapezeke mpaka lero kuchoka pa 11 Mrch pomwe mtembo wa gogoyu udapezeka.

murder

“Gogoyo ndi wa ku Chipata m’dziko la Zambia, m’mudzi mwa Tambala, koma adakwatirana ndi mwamuna wa ku Malawi Alubano Aaron Mbewe, wa zaka 63, wa m’mudzi mwa Kapita, T/A Mlonyeni ndipo amakhala m’malire a Zambia ndi Malawi,” adatero Nyirenda.

Mbewe adati wakhala pabanja ndi mayiyo kuyambira m’chaka cha 1976 mosangalala ndipo mkazi wakeyo ankatha kupita kwawo kukaona anthu nkubwerera popanda chovuta chilichonse kupatula patsikulo.

“Pa 10 March chaka chomwe chino adatsanzika kuti akupita kwawo kukatenga nkhuni koma sadabwerere mpaka tsiku lotsatiraro pa 11 March pomwe tidayamba kuda nkhawa,” adatero Mbewe.

Nyirenda adati mwana wa m’nyumbamo adayamba kuyang’ana mayi akewo pa 11 pomwepo ndipo mma 6 koloko madzulo adapeza mayi ake atagona chagada ali mbulanda m’kanjira mmphepete mwa munda wawo koma akuoneka kuti zamoyo palibe.

“Apolisi atapita pamalopo adapezadi mayiyo ali momwe mwanayo adafotokozera ndipo atatengera thupilo kuchipatala, adatsimikiza kuti malemuyo adgwiriridwa ndipo adafa kaamba kobanika achiwembuwo atamufinya pakhosi,” adatero Nyirenda.

Nduna yoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna ndi amayi, ana ndi okalamba Patricia Kaliati adadzudzula nkhanza zomwe gogoyo adachitiridwa ndipo wapempha apolisi kuti ayesetse kufufuza ndi kupeza omwe adachita chipongwecho.

Related Articles

Back to top button
Translate »