Nkhani

Akana ‘nyau’ yogwiririra

Listen to this article

Senior Chief Lukwa, mmodzi mwa mafumu akuluakulu a Achewa m’dziko muno, yemwenso amayankha pankhani za mafumu, wati munthu yemwe khothi m’boma la Dedza lidamupeza wolakwa pamlandu wogwiririra si wagulewamkulu monga momwe iye adakonzera kuti zioneke.

Khothi la Dedza, lomwe wogamula wake adali First Grade Magistrate Enett Banda, lidapeza Lazaro Maxwell, wa Zaka 19, wolakwa pamlandu wogwiririra mtsikana wa zaka 14 atadzizimbaitsa ngati gulewamkulu kuti asadziwike ndipo lidagamula kuti akagwire ndende yakalavulagaga kwa zaka 8.

Achewa amalemekeza gulewamkulu chifukwa ndi gule wa mizimu
Achewa amalemekeza gulewamkulu chifukwa ndi gule wa mizimu

Malingana ndi apolisi m’bomali, Maxwell adavomera mlanduwo m’bwalolo ndipo woimira boma pamlanduwo, Inspector Wedson Nyondo, adapempha bwalololo kuti lipereke chilango chokhwima kwa wopalamulayo kaamba koti woyimbidwa mlanduyo adanyozetsa chikhalidwe cha Achewa.

“Mpofunika kulingalira kuti munthuyu wanyazitsa chikhalidwe cha Achewa chomwe eni ake amateteza kuyambira kalekale kotero, n’kofunika kumpatsa chilango chokhwima kuti zotere zisamachitikechiteke,” adatero Nyondo.

Poperekapo maganizo ake pankhaniyi, Senior Chief Lukwa adati munthu yemwe adachita izi si wagulewamkulu yemwe amadziwika kuti ndi gule wa mizimu, koma munthu wazifukwa za mtopola wofuna kunyazitsa Achewa.

Lukwa: Umenewo ndi mtopola
Lukwa: Umenewo ndi mtopola

“Uwu ndiye timati mtopola. M’dziko muli khalidwe lolemekezana ndi kulemekezerana miyambo ndi zikhulupiriro zoyenera ndipo Mchewa weniweni sangachite zimenezi. Ameneyu ndi munthu wongofuna kuononga mbiri yabwino ya Achewa,” adatero Lukwa.

Iye adati khothi lomwe lidagamula mlanduwo lidachita bwino kumulanga chotero kuti iye ndi ena anzeru zangati zakezo atengerepo phunziro lolemekeza mitundu ndi miyambo a anthu.

Malingana ndi umboni umene udaperekedwa m’bwalo la milandulo, pa 8 mwezi womwe uno, Maxwell ndi mnzake wina yemwe sadatchulidwe adadziveka ngati gulewamkulu pomwe adakumana ndi msungwana wogwiririridwayo patchire lina lomwe limalekanitsa midzi ya Bowazulu ndi Kalipande.

Umboniwo udapitirira kenena kuti msungwanayo atangodutsana ndi gulewamkuluyo, Maxwell adayamba kumuthamangitsa ndipo atamugwira adamukokera patchire n’kumugwiririra.

Poti wogwiririrayo adali m’chigoba, msungwanayo adati munthu woyambirira kumuganizira adali Maxwell chifukwa adakhala akumuvutitsa kuti amamufuna chibwenzi koma amamukana ndipo nkhaniyi itafika kukhothi iye sadataye nthawi koma kuvomera mlanduwo.

Mlandu wogwiririra mwana wamng’ono umatsutsana ndi ndime 138 ya malamulo ogamulira milandu ndipo munthu akapezeka wolakwa, chilango chake chachikulu ndi zaka 14 akugwira ntchito yakalavula gaga kundende.

Maxwell amachokera m’mudzi mwa Chatondeza pomwe msungwanayo amachokera m’mudzi mwa Kalipande kwa T/A Chilikumwendo m’boma la Dedza.

 

Related Articles

Back to top button