Chichewa

Akapeza thanthwe pokumba manda zimatha bwanji?

Listen to this article

 

Zochitika kumanda nzambiri nthawi yokumba manda koma palibe nthawi yomwe adzukulu amakhaula kwambiri kuposa pamene apeza thanthwe dzenjelo lisadathe chifukwa sipakhala kusiya kuti akayambe pena. Uwu sumakhala ulesi, koma kuti ndi mwambo wake momwe zimayenera kukhalira. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi gulupu Mtwambwa wa ku Lilongwe yemwe akulongosola za mwambowu motere:

Mtwambwa: Kumakhala ngati  kuwayesa azimu
Mtwambwa: Kumakhala ngati
kuwayesa azimu

Mfumu, tiuzeni kuti ndinu yani?

Ndine Gulupu Mtwambwa ya m’dera la T/A Kalumba ndipo mtundu wathu ndi wa Achewa.

Mfumu, kumanda kumachitika zambiri adzukulu akamakumba koma chidandipatsako chidwi nchakuti akapeza mwala, mmalo mokwirira n’kukumba pena amapitiriza. Kodi n’chifukwa chiyani?

Ndi mwambo umene uja, sangayerekeze kusiya dzenje loyambayamba n’kuyambiranso lina chifukwa akhoza kukhala ndi mlandu waukulu m’mudzi moti akhoza kulipitsidwa chindapusa chachikulu kapena kusamutsidwa kumene m’mudzi atapanda kugonjera chigamulo cha akuluakulu.

Ndi mlandu wanji umenewu?

Umenewu ndi mlandu wolowetsa mphepo m’mudzi. Ife timakhulupirira kuti kuyamba kukumba dzenje n’kulilekeza panjira kuli ngati kukumba dzenje koma osaikamo maliro, zomwe zimapangitsa kuti anthu azipululuka chifukwa mizimu yakwiya kuti mwainamiza kuti kukubwera mmodzi mwa ana awo.

Si zongokhulupirira izi nanu Achewa?

Si zongokhulupirira, ayi, zimachitika. Ngakhale mutayenda kuno mpaka kufufuza m’manda simungapeze dzenje loyamba kukumbidwa kapena lomalizika kukumbidwa koma losaikamo mtembo. Zimenezi sizingatheke ndipo mfumu ya m’mudzi momwe mungachitike zotere yokha imadziwiratu kuti ikhoza kukhala pamoto waukulu.

Nanga thanthwelo likakhala lalikulu?

Basi adzukuluwo adziwa momwe achitire koma dzenjelo lipitirire basi mpaka lithe. Uthenga ukamabwera kumudzi kuti nyumba yatha kumanda, likhale kuti dzenjelo lakwanadi monga ndi momwe chikhalidwe chimanenera.

Si chilango kwa adzukulu chimenechi?

Ayinso, palibe za chilango. Kodi tiwalanga ngati abweretsa zovuta ndi iwowo bwanji? Munthu akamati akulowa m’gulu la adzukulu, amadziwiratu ntchito yomwe azikagwira kumeneko ndiye zonsezi amazidziwa kale, sizikhala zachilendo akakumana nazo.

Kapenatu mwina mumaona kuti malo angamathe msanga?

Ndinu nkhakamira. Moti monse muja simukumvabe kuti timatsatira mwambo momwe umayenera kukhalira? Ifensotu tidakhalako adzukulu ndipo zimenezi tidakumanapo nazo, sikuti zayamba lero. Tidazipeza, zikupitirira ndipo zidzakhalako mpaka kalekale.

Nanga akakhala kuti akumba poti padaikidwa kale munthu?

Apa pokha akhoza kufotsera nkuyamba pena, koma kuti mafumu adziwitsidwe ndipo akhale ndi umboni. N’zosavuta chifukwa mizimu singakwiye poti nayo imadziwa kuti alakwitsa, pamalopo padali kale nyumba ya wina.

Nanga zoti mtembo ukanyamuka subwerera m’nyumba zimatanthauzanji?

Nkhani yake ndi yofananirako chifukwa ponse pawiri timaopa kulowetsa mphepo pamudzi. Chokhacho chonyamula mtembo kumudzi kuti mukupita kokaika kumanda ndiye kuti mizimu kumeneko ikuchingamira ndiye kubwererera panjira, mizimu imakwiya kuti mwaipusitsa ndiye ikhoza kubwezera mowawa. Apa nchifukwa chake ngakhale mukumane ndi mvula yotani kaya ena amati kumanda kudabwera njuchi zobalalitsa anthu kumapezekabe kuti akuluakulu abwererako kukaika maliro chifukwa sangagone komanso sangabwerere kumudzi. n

Related Articles

Back to top button
Translate »