Nkhani

Akapizana madzi amoto poganizirana miseche

Listen to this article

Mayi wa zaka 21 Tionge Gerald ku Mponela m’boma la Dowa wakapiza madzi a moto mkazi mzake Lydia Tembo wa zaka 19 limodzi ndi mwana wake wa zaka zitatu pomuganizira kuti amamudya miseche.

Mneneri wapolisi ku Mponela a Kaitano Lubrino ati amayi awiriwo ndi a nyumba zoyandikana ndipo pa 26 April 2021, Gerald adamupeza mnzakeyo n’kuyamba kumufunsa ngati nzoona kuti iye amafalitsa zoti mnzakeyo ali ndi chibwenzi cha mseri.

Mayiyo adawazidwa madzi a moto

Iwo ati nkhaniyo idanyansa mnzakeyo mpaka awiriwo adayamba kukangana koma n’kuti Tembo panthawiyo atanyamula mwana wake wa zaka zitatu m’manja.

“Mkangano wawowo utatentha, Gerald adathamangira m’nyumba mwake n’kukatenga madzi a moto omwe adakapiza mnzakeyo ndi mwana yemwe ndipo onse adakupuka khungu,” adatero a Lubrino.

Iwo ati anthu a chifundo adakanena nkhaniyo kupolisi ndipo mayiyo limodzi ndi mwana wakeyo adatengeredwa kuchipatala chaching’ono cha Mponela komwe adalandira thandizo nkutuluka tsiku lomwelo.

A Kaitano adati Gerald atazindikira kuti wapalamula, adathawa m’mudzimo koma atamusaka adapezeka ndipo adamutsegulira mlandu wovulaza anthu womwe wumatsutsana ndi gawo 235 la malamulo a dziko la Malawi.

Iwo adati apolisi atamufunsa Gerald adati mnzakeyo amamunenera miseche kuti amazembera mwamuna wake ndi mwamuna wina ndipo adamuwona kumalo ena ogona alendo ndi mwamuna wachibwenziyo.

Pamsonkhano wotsegulira malo osamalirako anthu ozembetsedwa, nduna yoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo Patricia Kaliati adadzudzula amayi kuti asamachitane nkhanza okhaokha.

Iye adati amayi nthawi zambiri amakhala patsogolo kukadandaula kuti achitidwa nkhanza pomwe iwonso amakhala ndi mtima wankhanza ndi anzawo kapena ana aanzawo.

“Ngakhale Baibulo limanena kuti uzimpangira mnzako zomwe ungakondwe atakupangira iweyo, ndiye ngati amayi nokhanokha mukupangana nkhanza ndiye kuti mukupereka uthenga wanji kwa abambo? Aziti mumafuna nkhanza kaya,” adatero Kaliati.

Tembo amachokera m’mudzi mwa Nankumba, T/A Chakhaza m’boma la Dowa pomwe Gerald amachokera m’mudzi mwa Msampha, T/A Mponela m’boma la Dowa.

Related Articles

Back to top button