Nkhani

Akati ‘tonde azimveka fungo’ akutanthauzanji?

Miyambi ilipo yosiyanasiyana ndipo ina ukaimva mutu umachita kuwira, kulephera kulumikiza mwambiwo ndi tanthauzo lake. Ena amangoti bola ndanenapo mwambi osalingalira kuti kodi omvera akutengapo phunziro lanji pamwambiwo. Mwambi watitengera pabwaloli lero ndi wakuti “tonde azimveka fungo”. STEVEN PEMBAMOYO adakumana ndi mfumu Thipwi ya ku Nkhotakota kwa T/A Kanyenda pamsonkhano wokhudza za katetezedwe ka chilengedwe pomwe padatuluka mwambi wozunguawu ndipo adacheza motere:

Tied-u-goatsNdikudziweni, wawa.

Ine ndine Village Headman Thipwi wa m’dera la gogochalo Kanyenda m’boma lino la Nkhotakota.

Pamsonkhano walero mumabwerezabwereza mawu oti ‘tonde azimveka fungo’, mumatanthauzanji ndi mauwa?

Choyamba mudziwe kuti mawu amene aja ndi mwambi chabe ndiye monga mudziwa mwambi umanenedwa ndi cholinga choti omvera atengepo phunziro kapena chenjezo malingana ndi zomwe zachitika kapena zikuchitika.

Nanga poti pamsonkhano umeneuja padali anthu okhaokha padalibe mbuzi?

N’chifukwa chake mawuwo akutchedwa kuti mwambi, kutanthauza kuti sakuimira munthu aliyense, ayi, koma kuti pali phunziro lomwe tikufuna kuti anthu atolepo. Mwachitsanzo, msonkhano udali wokhudza za katetezedwe ka chilengedwe pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana ndiye mwambi umene uja udali woyenerera kuugwiritsa ntchito.

Nanga mwambiwu umatanthauzanji?

Chabwino, mwambi umenewu umatanthauza kuti ntchito zamanja za munthu ndizo zimamuchitira umboni. Ngati munthu ali wolimbikira, zotsatira za kulimbikira kwakeko zimafotokoza zambiri za iye popanda wina kuima pachulu n’kumalalika. Mwachitsanzo, mlimi wolimbikira amadziwika kuti ngolimbikira potengera zokolola zake, chimodzimodzi katswiri wa mpira wosewera kutsogolo amadziwika kaamba komwetsa zigoli.

Kutanthauza kuti mbuzi nchitsamba chabe chongobisalirako?

Ndi momwemo ndithu, sikuti timatanthauza kuti munthu yemwe tikukambayo ndi tonde poti akumveka fungo la mbuzi, ayi. Iyi ndi njira chabe yoperekera phunziro kapena malangizo ndi chilimbikitso moti apo anthu omwe adali pamsonkhanowu adziwa kuti aliyense pamenepanja azilingidwa ndi zotsatira za ntchito zake, osati kungokamba pakamwa, ayi.

Ndiye tonde zikumukhudza bwanji pamenepa, osasankha nyama zina bwanji?

Tondeyo ali ndi mbali yake yomwe amagwiritsidwira ntchito. Nkhani yaikulu ndi yakuti m’khola la mbuzi mukamabadwa ana pafupipafupi, ulemu umanka kwa tonde chifukwa ndiye amagwira ntchito mmenemo. Tonde

akakhala wolephera kapena kuti ofooka, khola limakhala pomwepomwepo asasuntha, ayi. Ndiye mlimi akaona kuti zaka zikutha mbuzi zake sizikuswana, amakabwerekera tonde wina, uja n’kumuchotsamo mwina kumugulitsa kwa mabutchala. Apa ndiye kuti amene uja sadamveke fungo chifukwa tonde mnzakeyo akangolowa m’khola n’kuyamba kubereketsa, amalandira matamando kuti ndiye tonde chifukwa zipatso zake zikuoneka.

Ndiye kuti aja amati akamva fwemba la munthu n’kumati tonde azimveka fungo amalakwitsa?

Kwambiri, chifukwa potero paja sipayenera kugwiritsidwa ntchito mwambi umenewu. Atapeza mwambi wina bola monga mwambi wakuti ‘wakumba kanyimbi’ chifukwa apo zikugwirizana poti kanyimbi naye ali ndi fungo vloboola m’mphuno osati masewera, ndiye ngati munthu akumveka fungo losakhala bwino monga mwaneneramo kuti fwemba ndiye kuti akuononga mpweya ndipo anzake akuzunzika ngati momwe amazunzira kanyimbi.

Pali miyambi ina yofanana tanthauzo ndi mwambi woti tonde azimveka fungo?

Miyambi ilipo yambirimbiri. Mwachitsanzo chabe, pali mwambi uja wakuti ‘langwani amaonekera kutali’ komanso ena amati chamuna chimaonekera poswa mphanje’ kutanthauza kuti zitakataka za munthu zimafotokoza ukatakwe kapena kufooka kwake. n

Related Articles

Back to top button