Nkhani

Akhazikitsa ntchito yolimbana ndi Edzi

Listen to this article

Boma mogwirizana ndi bungwe la Elizabeth Glaser Pediatric Aids Foundation ati ndondomeko yatsopano yolimbana ndi matenda a Edzi ya ndalama zokwana $4 miliyoni (zomwe ndizopitirira K1.6 billion) ithandiza kupulumutsa makanda 4 500 omwe akhoza kubadwa ndi kachilombo popanda ndondomekoyi.

Ndondomekoyi adaikhazikitsa pachipatala cha boma cha Mchinji kumapeto a sabata yathayi ndipo adati ntchito yoyendetsa ndondomekoyi iyamba m’maboma 7 ndipo ndalamazi n’zachaka chimodzi cha 2013.

Mkulu wa bungwe la Elizabeth Glazer Pediatric Aids Foundation Charles Lyons adati m’ndondomekoyi amayi 25 000 oyembekezera omwe ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi apeza mwayi wolandira mankhwala a Option B+ omwe amathandiza kuti mayi yemwe ali ndi kachilomboka asapatsire mwana wake pobadwa kapena kuyamwitsa.

Iye adati ntchitoyi ayikhazikitsa pofuna kukwaniritsa pangano la dziko lonse lapansi lofuna kuthetseratu kufala kwa kachilombo ka HIV kuchoka kwa mayi kupita kwa mwana pofika m’chaka cha 2015.

“Bungwe la Elizabeth Glazer Pediatric Aids Foundation lidayamba kugwira ntchito zake zolimbana ndi kufala kwa matenda a Edzi kuchoka kwa mayi kupita kwa mwana m’dziko muno zaka 12 zapitazo ndipo ena amakayika kuti ntchitozi zingathandize koma pano ambiri athandizika,” adatero Lyons.

Nduna ya zaumoyo, Catherine Gotani Hara, adati boma lidayamba kalekale ntchito zolimbana ndi matenda a Edzi koma chifukwa cha kukula kwa chiwerengero cha anthu omwe ali ndi kachilomboka poyerekeza ndi ndalama zogwirira ntchitoyi, ndi povuta kuti boma palokha lithane ndi mliriwu.

“Kwa zaka 30, kuchokera pomwe munthu woyamba adapezeka ndi kachirombo ka HIV m’dziko muno, boma lakhala likulimbana ndi kuthana ndi mliriwu koma pali nthawi zina zomwe unduna umalephera kukwaniritsa ntchitoyi chifukwa cha kuchulukwa kwa anthu ofuna nthandizo,” adatero Hara.

Wachiwiri kwa wamkulu wa ofesi ya Kazembe wa dziko la America Lisa Vickers wati ndondomeko yatsopanoyi ayiyendetsa ndi thandizo lochokela ku dziko la America kudzera m’bungwe la US President’s Emergency Plan for Aids Relief, United States Centers for Disease Control and Prevention (CDC), United States Agency for International Development ViiV Healthcare ndi mabungwe ena.

Iye adati ndondomekoyi ikukhudzaso kukonza kagwiridwe ntchito za chipatala m’zipatala za m’midzi pofuna kupititsa mtsogolo ntchito za umoyo komaso kuwonjezera chiwerengero cha anthu olandira ma ARV.

Related Articles

Back to top button