Nkhani

‘Akudyerera obwela’

Listen to this article

A malawi akhala akuingidwa ngati nkhuku m’maiko ena akafuna thandizo la chipatala, koma nzika zakunja kumadzawamwera mazira zikafika m’dziko muno ponama kuti ndi nzika za dziko lino.

Izitu zakhala zikuchitika chifukwa chosowa chiphaso cha unzika, koma lero mpumulo wafika kwa Amalawi pamene akhale ndi mwayi wokhala ndi chiphaso chosonyeza unzika wa dziko lino.

Kuthithikana m’zipatala zina kumadza chifukwa cha anthu a kunja
Kuthithikana m’zipatala zina kumadza chifukwa cha anthu a kunja

Zili chonchi malinga ndi ntchito yomwe bungwe la National Registration Bureau (NRB) poyamba kalembera wa unzika amene adayamba ndi akuluakulu aboma komanso maboma 11.

Monga akufotokozera Senior Chief Kanduku wa m’boma la Mwanza, boma lake limalandira nzika zambiri kuchokera m’dziko la Mozambique.

“Anthu pafupifupi atatu mwa 10 alionse amene amafuna thandizo lachipatala kuno amakhala a ku Mozambique. Vuto ndiloti kuyambira pa Zobue mpaka ku Tete m’dziko la Mozambique palibe chipatala, posowa kolowera, anthu adera limeneli amathandizidwa m’zipatala za dziko la Malawi,” adatero Kanduku.

“Ngakhale tayandikana ndi dzikolo, satilola kupita m’dziko lawo kukalandira thandizo la chipatala. Amalawi angapo akhala akuthamangitsidwa, ndipo suthandizidwa chifukwa anzathuwo ali ndi zitupa za unzika,” adaonjeza motero.

Naye Senior Chief Kabunduli ya m’boma la Nkhata Bay, adati kumeneko nzika za maiko a Tanzania zimalowa pafupifupi tsiku lililonse ndi kumalandira thandizo lomwe Amalawi amayenera kulandira.

“Akafika kuno amakhala ndi maina a Chimalawi zomwe ndizovuta kuwakaikira kuti si nzika zathu. Mankhwala pachipatala amatha mwachangu ife ndi kumavutika pamene iwo kwawo ali ndi zipatala zomwe zingawathandize,” adatero Kabunduli.

“Kungofika pa Chintheche pali anthu ambiri amaiko a Burundi, sangapitenso kwawo ndipo akulandira chithandizo chilichonse chomwe chimayenera chipite kwa Amalawi. Kwawo sungayerekeze kupanga zimenezi koma ifeyo amationa kupusa,” adaonjeza Kabunduli.

Kuti munthu ulandire thandizo lachipatala cha boma m’maiko monga Zambia, Zimbabwe, Mozambique ndi Tanzania, umayenera kuonetsa chitupa chosonyeza kuti ndiwe nzika koma kuno kwathu izi sizichitika chifukwa kulibe ziphasozi.

Monga akufotokozera Norman Fulatira yemwe ndi mneneri wa NRB, iyi mwina nkukhala mbiri yakale chifukwa Mmalawi weniweni azidziwika ndi chiphaso chomwe adulitse.

“Mavuto amenewa akhala mbiri yakale posakhalitsapa pamene ntchito yodula ziphaso za unzika yayamba. Gawo loyamba tayamba kupanga ziphaso za aphungu a Nyumba ya Malamulo, akuluakulu m’boma, komanso midzi 27 m’maboma 11,” adatero Fulatila.

Mabomawa ndi Chitipa, Mzimba, Nkhotakota, Lilongwe, Salima, Dowa, Mchinji, Blantyre, Mangochi, Chikwawa ndi Thyolo. Zitupazo azidula m’midzi iwiri pa boma lililonse.

“Ili ndi gawo loyamba, gawoli likufuna lingotithandiza momwe ntchito ikhalire, ili ngati ntchito yoyeserera kaye koma anthu alandira ziphaso zawo. Mudzi ulionse takonza zoyamba ndi anthu 200 ndipo gawoli likamatha, anthu 5 000 akhala ndi ziphaso zawo,” adatero mneneriyu.

Iye adati gawo lachiwiri la ntchitoyi, anthu 95 000 ndiwo adzakhale ndi mwayi wokhala ndi ziphasozi ndipo gawoli likuyembekezereka kudzatha mu December chaka chino.

Chaka chamawa, bungweli likuyembekezera kuti ntchitoyi idzafalikira dziko lonse pomwe anthu 9 miliyoni akuyembekezeka kulandira zitupa zawo.

Fulatira adati aliyense amene wakwanitsa zaka 15 ndiye akuyenera kudulitsa ziphasozi. Iye watinso ngati uli nzika ya dziko lino, uyenera kudulitsa ziphasozi posatengera zikhulupiriro zako kapena mpingo.

Naye mkulu wa bungwe loona zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe wati ntchitoyi ipindulira Amalawi komanso boma.

“Apapa ndiye kuti thandizo la mabungwe ndi boma lizipitadi m’manja mwa Amalawi enieni kusiyana ndi poyamba pamene timaphangirana ndi obwera,” adatero.

Kwa amene ataye chiphasochi akuti ayenera kudzalipira K3 500 kuti amupangirenso chiphaso china. Koma malinga ndi Fulatira, mtengowu ukhala ukusinthasintha.

Chiphasochi chizisiya kugwira ntchito pakatha zaka 10, kuchokera apo ndiye kuti mwini chiphasoyo azayenera kupangitsaso chiphaso china. n

Related Articles

Back to top button
Translate »