Nkhani

Akufuna ‘fisi’ alangidwe koopsa

 

Magulu omwe amalimbikitsa maufulu a amayi ati mpofunika mkulu woimira boma pa milandu Director of Public Prosecutions (DPP) Mary Kachale atengere nkhani ya Eric Aniva kubwalo lalikulu.

Aniva, yemwe adanjatidwa zaka ziwiri kukagwira ntchito ya kalavulagaga kundende atapezeka wolakwa pamlandu wotenga mbali pa miyambo yoopsa pokhala ‘fisi’ wochotsa fumbi ndi kulowa kufa m’boma la Nsanje.

Adampatsa zaka ziwiri: Aniva
Adampatsa zaka ziwiri: Aniva

Nkhani ya Aniva idagwedeza dziko atabwera poyera n’kuulula kuti wakhala akugwira ntchito ya ufisi kwa nthawi yaitali ndipo adagonana ndi amayi ndi atsikana oposa 100.

Koma magulu a amayi, motsogozedwa ndi mabungwe a Malawi Human Rights Resource Centre (MHRRC), NGO Gender Co-ordination Network (NGO-GCN) ndi African Women’s Development and Communications Network (Femnet), ati chigamulo chomwe Aniva adalandira lachiwiri lapitali n’chochepa.

Maguluwa ati potengera mlandu wa Aniva, ufulu wa amayi sudalemekezedwe kotero amayenera kulandira chilango chokhwima osati zaka ziwiri basi.

“Ndife okhudzidwa kuti munthu yemwe ali ndi kachilombo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a Edzi ndipo amapitiriza kugona ndi amayi ndi ana achichepere mpaka zaka 12 angalandire chilango chochepa chonchi.

“Ndi uthenga wanji omwe tikupereka kwa abambo ena akhalidwe longa lomweli? Zaka ziwiri basi mlandu wonsewu? Uku n’kunyoza amayi ndipo bwalo la milandu likuyenera kuunikapo bwino n’kusintha chigamulochi,” adatero mkulu wa bungwe la MHRRC Emma Kaliya.

Mabungwewa adati ngati nkhani yoyamba ya mtunduwu yoweruzidwa pogwiritsa ntchito lamulo latsopano la za ufulu wa anthu, Aniva amayenera kulandira chilango choletsa khalidweli.

Naye mkulu wa zophunzitsa anthu kubungwe la Femnet, Hellen Apila, adati apa dziko la Malawi waphonya mwayi waukulu wopera chenjezo kwa anthu omwe salemekeza ufulu wa amayi potsatila miyambo.

Bwalo la Magistrate ku Blantyre lidagamula Aniva lachiwiri lapitali kuti akagwire ntchito yakalavulagaga kundende atavomera kuti amachita mwambo wa fisi akudziwa kuti ali ndi kachilombo ka HIV.

Related Articles

Back to top button