Chichewa

Akufuna mayankho pa njala ya m’zipatala

Listen to this article

 

Mabungwe omwe si aboma ku Rumphi ati akudikirabe yankho kuchokera kwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pa zakusowa kwa chakudya m’zipatala zosiyanasiyana m’dziko muno.

Mwezi wathawu, mabungwe omwe ali pansi pa Civil Society Network ku Rumphi adachita zionetsero ngati njira imodzi youza boma kuti lichitepo kanthu pa zakusowa kwa chakudya pachipatala cha Rumphi.

Banda kuwerenga chikalata chomwe adalembera boma
Banda kuwerenga chikalata chomwe adalembera boma

Mabungwewa adauza Mutharika, kudzera m’chikalata chomwe adapereka kwa akuluakulu a boma, kuti awayankhe pasanadutse sabata ziwiri.

Wotsogolera mabungwewa, Eunice Banda, wauza Tamvani kuti boma silinayankhebe chikalata chawocho.

Iye wati mabungwewa akufuna kukhalanso pansi kuti apeze njira ina yopezera mayankho kuchokera ku boma.

“Titachita zionetsero boma lidapereka matumba 100 a chimanga. Koma chakudya chimenechi chitha kumapeto a mwezi uno. Izi zikutanthauza kuti kukhalanso njala kuyambira mwezi wamawa,” adatero Banda.

Nduna ya za masewero ndi chikhalidwe, Grace Chiumia, masiku apitawa adauza mabungwe kuti achepetse zionetsero chifukwa chakuti boma limamva kamodzi.

Chiumia, polankhula ku Nkhata Bay pamene amakhazikitsa ntchito zolimbana ndi nkhanza m’banja, adati ndalama zomwe mabungwe akugwiritsa ntchito pazionetsero azipititse kuntchito zachitukuko.

“Mabungwe achita zionetsero zokwanira. Ife ngati boma timamva kamodzi. Zinthu zikachulukitsa sizidyeka,” iwo adatero. n

Related Articles

Back to top button
Translate »